25-0928 Nthawi Yolumikizana Ndinso Chizindikiro

Uthenga: 63-0818 Nthawi Yolumikizana Ndinso Chizindikiro

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Mkwatibwi Wolumikizitsidwa,

Ndine wokondwa kwambiri, ndipo pansi pa chiyembekezero chachikulu chotero, kukhala gawo la zonse zomwe Mulungu akuchita mu tsiku lathu. Malingaliro a Mulungu pachiyambi tsopano akukwaniritsidwa pamaso pathu, ndipo ife ndife gawo la icho.

M’Baibulo lonse, aneneri analosera ndi kunena zimene zikanadzachitika. Nthawizina mauneneri amenewo sanakwaniritsidwe kwa mazana a zaka kenako, koma pamene chidzalo cha nthawi chinadza, icho chinafika pochitika; pakuti ganizo la Mulungu loyankhulidwa mwa mneneri wake liyenera kuchitika.

Mneneri Yesaya anati, “namwali adzaima.” Banja lililonse la Aheberi linakonzekeretsa mwana wawo wamkazi kuti abereke mwana. Iwo anagula izo nsapato ndi nsapato, ndi Birdseye wamng’ono, ndipo anakonzekera kuti mwanayo abwere. Mibadwo inapita, koma potsiriza Mawu a Mulungu anakwaniritsidwa.

Monga kamnyamata ine kakukula nthawizonse ndimadabwa, Ambuye, ine ndikuwona mu Mau anu kuti nthawi zonse mumagwirizanitsa anthu anu pamodzi kuti akwaniritse mawu anu. Munagwirizanitsa ana Anu Achihebri pamodzi mwa munthu mmodzi, Mose, amene anawatsogolera iwo ndi Lawi la Moto kupita ku Dziko Lolonjezedwa.

Pamene Inu munakhala thupi ndi kukhala pa dziko lapansi, Inu munagwirizanitsa ophunzira Anu. Inu munawalekanitsa iwo ku chirichonse ndi aliyense kuti awulule Mawu Anu kwa iwo. Pa tsiku la Pentekosite, munasonkhanitsanso Mpingo Wanu palimodzi pa malo amodzi, mu malingaliro amodzi ndi mtima umodzi musanabwere ndi kuwapatsa iwo Mzimu Woyera.

Ndinaganiza, zingatheke bwanji lero Ambuye? Mkwatibwi wanu wamwazikana padziko lonse lapansi. Kodi Mkwatibwi yense adzabwera ku Jeffersonville? Sindikuwona zomwe zikuchitika Ambuye. Koma Ambuye, Inu simumasintha dongosolo Lanu. Ndi Lamulo Lanu, palibe njira yoletsera. Inu muzichita motani izo?

ULEMERERO…LERO, tikhoza kuona ndi maso athu, ndipo koposa zonse, KHALANI GAWO LA ICHO: Mawu Amuyaya a Mulungu akukwaniritsidwa. Sitili MWATHUPI pamalo amodzi, tafalikira padziko lonse lapansi, koma Mzimu Woyera TSOPANO WALUMIKIZANITSA MKWATIBWI WAKE NDI MAWU A MULUNGU. MAWU AKE ANALANKHULIDWA NDIPO ANAJAMBULIDWA PA MATEPI, Mtheradi wa Mulungu wa lero, ukusonkhanitsa ndi KULUMIKIZANITSA MKWATIBWI WAKE… NDIPO PALIBE CHINACHILICHONSE CHINGAYIMITSE ICHO.

Mulungu akulumikizitsa Mkwatibwi Wake. Iye akubwera pamodzi, kuchokera Kummawa ndi Kumadzulo, ndi Kumpoto ndi Kummwera. Pali nthawi yolumikizana, ndipo iyo ikuchitika pakali pano. Kodi Iye akulumikizanira chiyani? Mkwatulo. Amen!

Nthawi yolumikizana ikuchitika PANO!!! Kodi chikutigwirizanitsa ndi chiyani? Mzimu Woyera mwa Mawu Ake, Liwu Lake. Kodi tikugwirizanitsa chiyani? MKWATULO!!! Ndipo tonse tikupita ndipo sitikusiya MMODZI kumbuyo.

Mulungu akumukonzekeretsa Iye. Inde bwana, kulumikizana! Kodi Iye akulumikizana ndi chiyani? Ndi Mawu!

Kodi Mawu amasiku ano ndi chiyani? UTHENGA uwu, MAWU AKE, Liwu la Mulungu kwa Mkwatibwi Wake. Osati mwamuna. Osati amuna. Osati gulu. Otsimikiziridwa, ndi Lawi la Moto, MAWU a Mulungu pa matepi.

“Pakuti miyamba yonse ndi dziko lapansi zidzapita, koma Mawu Anga sadzapita.” Iye akudzilumikizitsa Iyemwini ndi PAKUTI ATERO AMBUYE mosalabadila zimene chipembedzo chirichonse kapena wina aliyenseyo akunena.

Mosasamala chimene ALIYENSE anena, ife tikulumikizana ndi zotsimikiziridwa, zotsimikiziridwa, Atero Liwu la Ambuye la tsiku lathu. Osati kutanthauzira kwa wina; tingachite bwanji zimenezo? Izo zimasintha ndi munthu aliyense, koma Liwu la Mulungu pa matepi SALISINTHA ndipo Ilo lalengezedwa ndi Lawi la Moto Lokha kuti ndi Mawu a Mulungu ndi Liwu la Mulungu.

Vuto lake ndi lakuti, ndi munthu, iye samamudziwa mtsogoleri wake. Inde, bwana. Iwo amasonkhanira chipembedzo, iwo amamusonkhanira bishopu kapena munthu, koma iwo sangamusonkhanire Mtsogoleri, Mzimu Woyera mu Mawu. Mukuona? Iwo amati, “O, chabwino, ine ndikuwopa ine ndikhala wotengeka pang’ono; ine ndikuwopa ine ndiponda phazi lolakwika.” Ohhhh, ndi zimenezotu!

Apa ndi pamene otsutsa amalozera kwa mipingo yawo ndi kuti, “Onani, iwo akukwezera mmwamba munthu, M’bale Branham.

Zachabechabe, tikulumikizana mozungulira MAWU OYENZEDWA A MULUNGU OLANKHULIDWA KUPYOLERA MUNTHU UYO. Kumbukirani, ameneyo ndi mwamuna yemwe Mulungu anamusankha kuti akhale Liwu Lake kuti aitane ndi kutsogolera Mkwatibwi Wake mu tsiku lino. Limenelo ndi Liwu LOKHALA lotsimikiziridwa ndi Mulungu Mwiniwake.

Koma mophonya , IWO akulumikizana mozungulira ANTHU. Iwo sakusewera Liwu la Mulungu pa matepi mu mipingo yawo. Kodi inu mungaganize moteromo??? Mtumiki amene amadzinenera kuti akukhulupirira Uthenga uwu kuti ndi Uthenga wa nthawi ino, pakuti Atero Ambuye, koma akupeza chowiringula chamtundu wina choti SANGAKHOZE kusewera Liwu limenelo mu mipingo yawo, koma azitumikira kwa anthu iwo AYENERA kumvetsera kwa iwo ndi atumiki ena akulalikira Mawu… ndiye amati ife tikutsatira munthu!!!

Tangomva Lamulungu lapitali zomwe Mulungu anawachitira amuna amenewo!!

Tikukonzekera Ukwati. Ife tikukhala Mmodzi ndi Iye. Mawu amakhala inu, ndipo inu mumakhala Mawu. Yesu anati, “Pa tsiku limenelo inu mudzadziwa izo. Onse Atate ali, Ine ndine; ndipo zonse Ine ndiri, inu muli; ndipo nonse inu muli, Ine ndiri. Mu tsiku limenelo inu mudzadziwa kuti Ine ndiri mwa Atate, Atate mwa Ine, Ine mwa inu, ndi inu mwa Ine.”

Zikomo Ambuye chifukwa cha Vumbulutso la Inu Nokha, ndi ifeeni, mu tsiku lathu. Mkwatibwi Wanu podzikonzekeretsa Yekha ndi Mawu Anu Olankhulidwa. Tikudziwa kuti tili mu Chifuniro Chanu changwiro pakukhala ndi Mawu Anu olembedwa.

Ndikuitana dziko kuti limvetsere ku Liwu lokhalo lotsimikiziridwa la Mulungu la tsiku lathu Lamulungu lino. Muli wolandiridwa kulumikizana nafe Lamulungu nthawi ya 12:00 p.m., nthawi ya ku Jeffersonville, pomwe tikumvera: 63-0818, Nthawi Yolumikizana Ndinso Chizindikiro . Ngati simungathe kulumikizana ndi kumvetsera nafe, sankhani tepi, TEPI ILIYONSE; iwo onse ali pakuti Atero Ambuye, ndipo mvetserani ku Mawu a Mulungu kukupangani inu kukhala angwiro ndi kukupangani inu kukonzekera kubwera Kwake posachedwa.

M’bale. Joseph Branham

Masalimo 86:1-11
Mateyu 16:1-3

Iye akudzilumikizitsa Iyemwini. Iye akukonzekera. Chifukwa chiyani? Iye ndi Mkwatibwi. Uko nkulondola. Ndipo Iye akudzilumikizitsa Iyemwini ndi Mkwati Wake, mwaona, ndipo Mkwati ndi Mawu. “Pachiyambi panali Mawu, Mawu anali ndi Mulungu, ndipo Mawu anali Mulungu. Ndipo Mawu anasandulika thupi ndipo anadzakhala pakati pathu.”