Uthenga: 63-0707M Chitsutso
Okondedwa Iwo Omasulidwa,
Tsopano, kumeneko, “iwo,” osati wochimwa. “Iwo,” amenewo ndi, mpingo wa tsiku limenelo, iwo anapeza cholakwika ndi Munthu Yemwe anali Mawu. Ndi kulondola uko? Iwo anapeza cholakwika ndi Munthu Yemwe anali Mawu. Tsopano iwo akupeza cholakwika ndi Mawu akugwira ntchito kupyolera mwa munthu.
Kuyambira pachiyambi dziko lamukana Iye, linamukana Iye, linakana kukhala ndi Mawu Ake pa kusunga ndi miyambo yawo, zikhulupiriro zawo, malingaliro awo. Iwo nthawizonse amaphonya dongosolo la Mulungu; Mulungu, monga Munthu, yemwe anali Mawu, ndipo tsopano Mawu akugwira ntchito kupyolera mwa munthu.
Koma mu tsiku lathu Iye anati, “Ine ndidzakhala nawo gulu laling’ono, osankhidwa apang’ono, iwo anali mwa Ine kuchokera pachiyambi. Iwo adzandilandila Ine ndi kudzakhulupilira mau anga ndi Munthu yemwe Ine ndinamusankha kudzaulula mau anga. Iye adzakhala Liwu Langa kwa iwo
“Iwo sadzachita manyazi kulalikira Liwu Langa.” Iwo sadzachita manyazi kuuza dziko kuti Ine ndabwera kachiwiri ndipo ndadziwonetsera Ndekha kupyolera mu thupi la munthu monga Ine ndinanenera kuti Ine ndidzachita. Nthawi imeneyi iwo sadzamupembedza munthuyo, koma iwo azidzandipembedza Ine, Mawu, amene ati adzayankhule kupyolera mwa munthu. Adzandikonda Ine ndi kundilengeza mu m’tsempha uliwonse wa umunthu wawo.”
“Potero, Ine ndawapatsa iwo zonse zomwe iwo akusowa kuti akhale Mkwatibwi Wanga. Ine ndawalimbitsa iwo ndi Mawu Anga; pakuti iwo ALI MAWU ANGA atasandulika thupi. Ngati iwo akusowa machiritso, iwo alankhule Mawu Anga. Ngati iwo ali ndi chotchinga chirichonse chimene chimawatchinga iwo, iwo alankhule Mawu Anga. Ngati iwo ali ndi mwana yemwe walowelela, iwo alankhule Mawu Anga. Chirichonse chimene iwo akusowa, iwo alankhule Mawu Anga, pakuti iwo ali Mawu Anga opangidwa thupi mwa iwo.”
“Iwo akudziwa omwe iwo ali, pakuti Ine ndadziululira Inemwini kwa iwo. Iwo akhala owona ndi okhulupirika ku Mawu Anga ndipo akulumikizana palimodzi kuzungulira Liwu Langa.Pakuti iwo akudziwa Liwu Langa, Mawu Anga, Mzimu Wanga Woyera. Iwo akudziwa, kumene kuli Mawu, Mphungu zidzasonkhanitsidwa.”
Pamene mneneri Wake akulankhula Mawu Ake ndi kuwutsutsa m’badwo uno wa kumupachika Yesu Khristu kachiwiri ndi kulengeza kuti iwo awonongedwa, Mkwatibwi adzakhala akusangalala. Pakuti ife tikudziwa IFE NDIFE Mkwatibwi Wake yemwe wawavomereza ndi kuwalandira Mawu Ake. Timafuula kuchokera pansi pamtima kuti:
Ndine Wanu, Ambuye. Ine ndikudzigoneka ndekha pa guwa ili, basi modzipatula monga ine ndikudziwira kuti ndidzipange ndekha. Tengani dziko lichoke mwa ine, Ambuye. Tengani zinthu kuchokera kwa ine zomwe ziri zakutha; ndipatseni ine zinthu zosatha, Mawu a Mulungu. Mundirole ine ndikhoze kumakhala moyo Mawu amenewo mwapafupi kwambiri, mpaka Mawu akhale ali mwa ine, ndi ine mu Mawu. Perekani izi Ambuye. Mundirole ine ndisadzachoke konse kwa Iwo.
Pali moyo, ndipo pali imfa. Pali njira yolondola, ndipo pali njira yolakwika. Pali choonadi, ndipo pali bodza. Uthenga uwu, Liwu ili, ndi njira yangwiro yoperekedwa ndi Mulungu ya lero. Bwerani mudzajowine gawo la Mkwatibwi wamphamvu wa Mulungu pamene tikusonkhana mozungulira Mawu Ake owululidwa ndi kumva Uthenga: Chitsutso 63-0707M.
M’bale. Joseph Branham