25-0914 Kodi Moyo Wanu Ndi Woyenera Uthenga?

Uthenga: 63-0630E Kodi Moyo Wanu Ndi Woyenera Uthenga?

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa Abale ndi Alongo,

Ine ndimawakonda Ambuye, Mawu a Mulungu, Uthenga uwu, Liwu Lake, mneneri Wake, Mkwatibwi Wake, kuposa moyo iwomwini. Onse ali MMODZI KWA INE. Ine sindikufuna konse kunyengerera pa cholemba chimodzi, kachidutswa kamodzi, kapena MAWU AMODZI amene Mulungu anawalemba mu Mawu Ake kapena anayankhula kupyolera mwa mneneri Wake. Kwa ine, Zonse ndi Atero Yehova.

Mulungu ankaganiza Izo, ndiye anayankhula Izo kwa aneneri Ake, ndipo iwo analemba Mawu Ake. Ndiye Iye anatumiza mngelo Wake wamphamvu, William Marrion Branham, ku dziko lapansi mu tsiku lathu kotero kuti Iye akhoze kudziulula Yekha mu thupi la munthu kamodzinso, monga Iye anachitira ndi Abrahamu. Ndiye Iye analankhula kupyolera mwa mneneri Wake kuti akhale Liwu la Mulungu kwa dziko, kuti awulule ndi kutanthauzira zinsinsi zonse zimene zabisika kuchokera ku maziko a dziko kwa Mkwatibwi Wake wokonzedweratu.

Tsopano, Mkwatibwi Wake, INU, mukukhala Mawu osandulika thupi; Mmodzi ndi Iye, Mkwatibwi Wake wa Mawu wobwezeretsedwa kwathunthu.

Ndikudziwa kuti sindikumvetsetsa zomwe ndikunena komanso zomwe ndimalemba. Ndiloleni ndinene modzichepetsa monga momwe mneneri wathu ananenera, sindine wophunzira ndipo ndikudziwa kuti sindingathe kulemba kapena kulankhula molondola zimene ndikumva mumtima mwanga. Ndikuvomereza kuti zikuwoneka ngati ndimalemba mwawukali nthawi zina. Pamene nditero, sikusonyeza kupanda ulemu, kapena kukhala ndi maganizo olakwika kapena kuweruza wina, koma mosiyana. Ndimachita izi chifukwa chokonda Mawu a Mulungu mumtima mwanga.

Ine ndikufuna kuti aliyense avomereze ndi kukhulupirira Uthenga uwu umene Mulungu anatumiza kudzayitana Mkwatibwi Wake. Sindinamvepo mumtima mwanga kapena malingaliro anga kuti atumiki sayenera kulalikiranso; zikanakhala zikutsutsana ndi Mawu a Mulungu. Ndine wachangu chabe pa Mau a Mulungu pa matepi. Ine ndikukhulupirira kuti ndilo Liwu lofunika kwambiri lomwe ATUMIKI ONSE ayenera kuyika POYAMBA pamaso pa anthu. Izi sizikutanthauza kuti sangathe kulalikira, ndikungofuna kuwalimbikitsa kuti azisewera matepi mu mipingo yawo pamene anthu asonkhana pansi pa kudzoza kumeneko.

Inde, ndikanakonda kukhala ndi dziko lonse lapansi likumvetsera Uthenga womwewo nthawi imodzi padziko lonse lapansi. Osati chifukwa “ine” ndinanena chomwecho, kapena chifukwa “Ine” ndinasankha tepi kuti ndimvetsereko, koma ine ndikumverera ndithudi Mkwatibwi akanawona momwe Mulungu wakonzera njira kuti izi zichitike mu tsiku lathu.

Ngati ife tikanakhala nazo zojambulidwa za Yesu akuyankhula lero pa tepi, osati Mateyu, Marko, Luka kapena zolemba za Yohane za zomwe Yesu ananena (pakuti iwo onse ananena izo mosiyana pang’ono), koma nkumakhoza kumva Liwu la Yesu, umunthu Wake, makutu Ake, ndi makutu athu omwe, kodi utumiki lero unganene kwa mpingo wawo, “Ife sitidzasewera zojambulidwa za Yesu kuti ndizilalikira kwa Inu ndi kudzozedwa kwa izo mu mpingo wathu. Ine ndi woyitanidwa ndi odzozedwa kuwulalikira Iwo ndikumaubwereza iwo. Inu basi muzikavetsera ku Iwo mukapita kunyumba kwanu.” Kodi anthu angakhoze kumayima ndi zimenezo? N’zomvetsa chisoni kuziyankhula kuti zimenezi ndendende n’zimene akuchita lero lino. PALIBE KUSIYANA, ziribe kanthu momwe Iwo amachipanga icho kukhala choyera.

Kwa ine, M’bale Branham anatipatsa ife chitsanzo. Iye ankakonda pamene mipingo yonse, nyumba, kapena kulikonse kumene iwo anali, anali pa kulumikizana kotero kuti iwo azitha kumva Uthenga onse nthawi imodzi. Iye ankadziwa kuti iwo akanakhoza, ndipo akanati, awatenge matepi ndi kuwamva iwo kenako, koma iye ankawafuna iwo kuti akhale olumikizana ndi kumamva Uthenga onse pa nthawi imodzi…. KWA INE UMO NDIMOMWE ANALILI MULUNGU AKUSONYEZA MKWATIBWI WAKE MOMWE ZIDZAKHALIRE MU TSIKU LATHU NDI ZOYENERA KUCHITA.

Mtumiki woona aliyense wokhulupirira Uthenga adzavomereza kuti palibe chachikulu kuposa kukhala pansi pa kudzoza kwa Liwu la Mulungu, limene linajambulidwa ndi kuikidwa pa matepi. Mkwatibwi adzakhulupirira, ndi kukhala ndi Vumbulutso, kuti Uthenga uwu ndi Mawu a Mulungu a lero. Ine ndikhoza kungoweruza ndi Mawu, koma aliyense amene sakanati Uthenga uwu uli Mtheradi wawo alibe Vumbulutso la Mawu la lero, chotero, iwo angakhoze bwanji kukhala Mkwatibwi Wake?

Sikuti kumangobwereza izo, kulalikira kapena kuziphunzitsa izo, koma kuzimva izo pa matepi ndi MALO OKHAWO omwe Mkwatibwi anganene kuti ine ndimakhulupirira Mawu aliwonse. Uthenga uwu uli PAKUTI ATERO AMBUYE. Chimene ine ndimalalikira kapena kuphunzitsa si PAKUTI ATERO AMBUYE, koma chimene Liwu la Mulungu limanena pa matepi CHILI…

Ine ndikudziwa alipo abale ndi alongo amene amati, ndi kumverera, “Ngati inu simukumvera Uthenga wa Branham Tabernacle nsanamira, kuwerenga makalata a Mphungu Zikusonkhana, ndi kumamvetsera mnyumba zanu pa nthawi yomweyo inu simuli Mkwatibwi,” kapena, “Ndi kulakwa kupita ku tchalitchi, inu muyenera kukhala mnyumba mwanu.” NDIKULAKWA KWAMBIRI. Ine sindinayambe ndaganizapo zimenezo, kunena izo, kapena kukhulupirira izo. Izo zapangitsa ngakhale kupatukana kochuluka, zomverera zolimba, ndi kuchotsedwa pakati pa Mkwatibwi ndipo mdani akugwiritsa ntchito izo kuwalekanitsa anthu.

Ine sindikufuna konse kumulekanitsa Mkwatibwi, ine ndikufuna kuti ndimulumikize Mkwatibwi monga Mawu ananenera TIYENERA KUKHALA WOLUMIKIZANA NGATI MMODZI. Ife tisamakangane wina ndi mzake, koma palibenso china mophweka chimene chingatilumikizitse ife koma Liwu la Mulungu pa matepi.

Ife Sitiyenera kumakangana ndikuuza anthu zomwe AYENERA KUCHITA kapena kuti iwo si Mkwatibwi, inuyo ingochitani monga AMBUYE AKUKUTSOGOLERANI. Iwo akali abale ndi alongo athu. Tifunika kukondana ndi kulemekezana.

Tsopano, musakangane. Mwaona? Kupsa mtima kumabweretsa mkwiyo. Chinthu choyamba inu mukudziwa, inu mukukwiyitsa Mzimu Woyera kuchoka kwa inu, inu mudzakhala mukukangana mobwezera. Ndiye Mzimu Woyera umayamba kuwuluka. Kupsa mtima kumabweretsa mkwiyo.

Ndi zimene mneneri ananena apa, ine sindikufuna konse kumvetsa chisoni Mzimu Woyera. Sindikufuna kukangana. Titha kukambirana mwachikondi, koma osati kukangana. Ngati ndalankhula chilichonse chomwe chakhumudwitsa wina aliyense mu zomwe ndalemba kapena kunena, ndikhululukireni, sichinali cholinga changa.

Monga ndanenera kale, ndikumva kuitana pa moyo wanga kuchokera kwa Ambuye kuti ndilole anthu ku Mawu a Mulungu lero. Atumiki ena ali ndi maitanidwe ena ndipo mwina amawona zinthu mosiyana. Utumiki wanga ndi kungomuuza Mkwatibwi kuti, “KUKANIKIZA KUSEWERA” ndi “Liwu la Mulungu pa matepi ndilo Liwu lofunika kwambiri limene mungamve.” “Ine ndikukhulupirira kuti utumiki uyenera kumasewera Liwu la Mulungu pa matepi mu mipingo yawo.”

Makalata amene ine ndimalemba sabata iliyonse ndi a gawo la Mkwatibwi amene amadzimva kuti ali gawo la Branham Tabernacle. Ndikudziwa kuti ena ambiri amawawerenga, koma ndili ndi udindo wochita zomwe ndikumverera kuchitidwa mu tchalitchi chathu. Mpingo uliwonse uli wa pawokha; iwo ayenera kuchita monga iwo akumverera kutsogozedwa ndi Ambuye kuti achite, ndiwo 100% Mawu. Ine Sindikutsutsana nawo iwo, timangosagwirizana. Kwa ine ndi Branham Tabernacle, ife tikungofuna kokha basi kuti tizimva Liwu la Mulungu pa matepi.

Ine Ndimaitana dziko kuti lizijowinana nafe sabata iliyonse. Ndimawalimbikitsa kuti ngati sangathe kujowinana nafe, kusankha tepi, tepi iliyonse, ndikuyikanikiza kuisewera iyo. Iwo adzadzozedwa kuposa kale. Kotero, ine ndikukuitanani inu sabata ino kuti mudzajowinane nafe Lamlungu pa 12:00 P.M., nthawi ya ku Jeffersonville, pamene ife tidzasonkhana pamodzi ndi kumva, 63-0630E Kodi Moyo Wanu Ndi Woyenera Uthenga?

M’bale Joseph Branham