25-0831 Ukulirira Chiyani? Yankhula!

Uthenga: 63-0714M Ukulirira Chiyani? Yankhula!

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Mpingo wa Mulungu,

Mulungu analankhula nati, ““Ine sindigwira ntchito pa dziko lapansi, kupatula kupyolera mwa munthu. Ine—Ine—Ine ndine Mpesa; inu ndinu nthambi. Ndipo ine ndimadzifotokoza kokha Inemwini pamene ine ndingakhoze kupeza munthu M’MODZI. Ndipo Ine ndamusankha iye, William Marrion Branham. Ine ndamutumiza iye kumusi kuti adzaitane Mkwatibwi Wanga. Ine ndidzaika Mau anga mu mkamwa mwake . Mau anga adzakhala Mau ake. Iye adzalankhula Mau anga ndi kumalankhula zokhazo zomwe ine ndimalankhula.

Liwu la Lemba linayankhula kupyolera mu Lawi la Moto ndipo linamuuza iye, “Ine ndakusankha iwe, William Branham. Iwe ndi mwamunayo. Ine ndinakulera iwe kwa cholinga ichi. Ine ndidzakutsimikizira iwe mwa zizindikiro ndi zodabwitsa. Iwe ukupita ku dziko la pansi kuti ukaulule Mawu Anga ndi kukamutsogolera Mkwatibwi Wanga. Mawu Anga ayenera kuti akwaniritsidwe ndi IWE.”

Mneneri wathu ankadziwa kuti anatumidwa ndi cholinga chomwecho kuti aulule zinsinsi zonse za Baibulo ndi kutsogolera Mkwatibwi wa Mulungu ku Dziko Lolonjezedwa. Iye ankadziwa chimene iye ananena, Mulungu akanadzalemekeza ndi kuchikwaniritsa. Ine ndikufuna kuti inu musamaiwale Mawu amenewo. Zimene mneneri wathu ananena, Mulungu azilemekeza, chifukwa Mawu a Mulungu anali mwa William Marrion Branham. Iye ali Liwu la Mulungu kwa dziko.

Iye ankadziwa kuti iye anali mngelo wodzozedwa wa Mulungu. Iye ankadziwa mumtima mwake zonse zimene Mulungu ananena zokhudza iye m’Mawu ake. Zomwe zinkamudetsa nkhawa kwambiri zinali zitachitikadi. Iye anali wodzozedwa ndipo ankadziwa kuti iye anali ndi PAKUTI ATERO AMBUYE. Palibe chimene chikanamuletsa kupita kukalankhula Mawu a Mulungu.

Mulungu anamuuza iye, “Mawu Anga, ndi iweyo, Mtumiki Wanga, muli ofanana.” Iye ankadziwa kuti iye ndi amene anasankhidwa kulankhula Mawu osalephera. Ndizo zonse zomwe iye adafunitsitsa. Iye AMATHA KUYANKHUL A, NDIPO MULUNGU ANKACHITITSA ICHO KUKWANILITSIDWA.

Vumbulutso la Uthenga uwu NDI mthenga wa Mulungu wadzoza chikhulupiriro chathu KUPOSA momwe zisanachitikepo mkale lonse. Izo zatisunthira ife mu magulu aakulu kwambiri. Izo zatilekanitsa ife ku chirichonse kupatula Uthenga Wake, Mawu Ake, Liwu Lake, Matepi Ake.

Ziribe kanthu kuti ndife ochepa bwanji, timasekedwa mochuluka bwanji, kunyozedwa, sizimatitekesa mpang’ono pomwe. IFE TIMACHIONA ICHO. IFE TIMAKHULUPIRIRA ICHO. Pali chinachake mkati mwathu. Tinakonzedweratu kuti tidzachiwone ICHO ndipo palibe chimene chidzaatilepheretsa ife kuchikhulupirira ICHO.

Ife timakumbukira zomwe masomphenyawo ananena, “bwerera ukasunge Chakudya”. Kodi nkhokweyo inali kuti? Branham Tabernacle. Kodi pali chirichonse mu dziko, kapena kuzungulira dziko kulikonse, chimene chingafanane ndi Mauthenga amene ife tiri nawo? IWO ndi Liwu lokhalo lotsimikiziridwa ndi Mulungu Mwiniwake kuti liri PAKUTI ATERO AMBUYE. LIWU LOKHALO!

Kodi ndi kutiso kumene ife tikanati, kapena tikanafuna kupita, pamene iye anati;

Apa ndi pomwe Chakudyachi chasungidwira…

Icho chasungidwa pano
Iwo uli pa matepi. Iwo uzipita ku kutambalala konse kwa dziko pa matepi, kumene anthu mu manyumba mwawo. Matepi amenewo azikafika mmanja mwa a okonzedweratu a Mulungu. Iye akhoza kuwalondolera Mawu. Iye alondolera chirichonse ndendende basi mpaka ku ntchito yake. Ndicho chifukwa Iye ananditumiza Ine kuti ndibwerere ndidzachite izi. “Kudzachisunga Chakudyacho kuno.”

Ife Ndife Mkwatibwi wa Mawu Ake Angwiro amene wakhala ndi Chakudya Chake Chosungidwa. Palibe chifukwa chomaliranso, ife timangoyankhula Mawu ndi kupita patsogolo, pakuti ife NDIFE Mawu.

Palibe chomadela nkhawa. Palibeso chifukwa chomakhalira ndi misonkhano ya mapemphero ausiku onse kuti itiwululire kuti ife ndife ndani, Mawu avumbulutsidwa kwa ife. Timadziwa kuti ndife ndani, mofanana ndi mneneri wa Mulungu, ndipo watiuza kale amene anali kupita.

“Mmodzi aliyense wa ife! Kaya ndinu mkazi wa mnyumba, kapena ndinu m—mdzakazi wamng’ono, kapena ndinu mkazi wachikulire, kapena mwamuna wamng’ono, kapena mwamuna wachikulire, kapena chirichonse chimene inu muli, ife tikupita, mulimonse. Sipakhala mmodzi wa ife ati atsalire.” Ameni. “Mmodzi aliyense wa ife akupita, ndipo ife sitiletsa kanthu kalikonse.”

Lankhulani za kutipatsa ife CHIKHULUPILIRO chokwatulitsa!!!

Bwerani mudzajowine gawo la Mkwatibwi wa Mulungu pamene ife tikusonkhana palimodzi mozungulira Liwu lotsimikiziridwa la Mulungu, pamene Iye akuyankhula ndi kutiuza ife: Wokondedwa Wanga, Wosankhidwa Wanga, Mkwatibwi Wanga, Ukulilira Chiyani, Yankhula, ndipo pita patsogolo.

M’bale. Joseph Branham

Uthenga: 63-0714M Ukulilira Chiyani? Yankhula!

Nthawi: 12:00 PM, Nthawi yaku Jeffersonville

Malo:

Koma pali Mpingo weniweni umodzi wokha, ndipo iwe sumajowina Iwo. Iwe umabadwira mwa Iwo. Mwaona? Ndipo ngati iwe wabadwira mwa iwo, Mulungu wamoyo amagwira ntchito Iyemwini kupyolera iwe, ndi kumadzipangitsa Iyemwini kudziwika. Mwaona? Ndiko kumene Mulungu amakhala, mu Mpingo Wake. Mulungu amapita ku Tchalitchi tsiku lirilonse, amakhala moyo mu Mpingo. Iye amakhala moyo mwa inu. Inu ndinu Mpingo Wake. Inu ndinu Mpingo Wake. Inu ndinu Kachisi amene Mulungu amakhalamo. Ndinu Mpingo wa Mulungu wamoyo, inueni.