Uthenga: 65-1206 Zochitika Zamakono Zimamveka Bwino Ndi Uneneri
- 25-0810 Zochitika Zamakono Zimamveka Bwino Ndi Uneneri
- 21-1206 Zochitika Zamakono Zimamveka Bwino Ndi Uneneri
- 20-0726 Zochitika Zamakono Zimamveka Bwino Ndi Uneneri
- 18-0121 Zochitika Zamakono Zimamveka Bwino Ndi Uneneri
- 15-1207 Zochitika Zamakono Zimamveka Bwino Ndi Uneneri
Wokondedwa Mkwatibwi Woona ndi Wamoyo,
Pamene Yesu, Mawu Iwoeni, anabwera ku dziko lapansi zaka 2000 zapitazo, Iye anabwera monga Iye ananenera kuti Iye akanadzabwera, monga Mneneri. Mawu Ake amalengeza, kuti Iye asanabwere kachiwiri, mawonetseredwe athunthu a Umunthu wa Yesu Khristu adzawonetseredwa kachiwiri mu thupi, mwa mneneri. Mneneri ameneyo wabwera, dzina lake ndi William Marrion Branham.
Kodi wina aliyense angalephere bwanji kuzindikira kuti kumvera Liwu la Mulungu kumalankhula ndi iwo mwachindunji pa matepi kuti ndicho Chifuniro changwiro cha Mulungu? Ife tikudziwa kuti Mawu nthawizonse amadza kwa mneneri Wake; Sizingabwere mwanjira ina iliyonse. Izo ziyenera kubwera kupyolera mu njira ya Mulungu imene Iye anatiwuziratu kale za iyo . Ndi njira yokhayo yomwe Izo zidzadzere konse. Mulungu amayenda mu njira imene Iye analonjeza kuti Iye akanadzachita izo. Iye samalephera konse kuchita izo mwanjira yomweyo yofanana momwe Iye nthawizonse ankachitira.
Wina aliyense wa iwo ankadya chinthu chomwecho, iwo onse ankavina mu Mzimu, iwo onse anali nacho chirichonse mofanana; koma pamene izo zinafika ku nthawi yolekanitsidwa, Mawu ndi omwe analekanitsa. Mmomwe izo zirili lero! Mawu ndi omwe amalekanitsa! Pamene ifika nthawi yake,
Ife tikuwona kuti nthawi ikuchitika tsopano, Mawu akulekanitsa. Mkwatibwi akuimbidwa mlandu wa kuyika zochuluka kwambiri pa mneneri pamene iwo amati, “Pali amuna ena oyitanidwa ndi Mulungu, odzazidwa ndi Mzimu Woyera kuti atsogolere Mkwatibwi lero.” Inu mukusowa zochuluka kuposa matepi okha.Mulungu wayika amuna lero kuti atsogolere mpingo
“Iwe ukuyesera kumaganiza kuti ndiwe mmodzi wekha bwinoko kuposa izo. Ndipo iye anati, “Chabwino, gulu lonseli ndi loyera. Iwe ukuyesera kumadzipanga wekha…” Ngati ife tikanati tinene izo lero, kayankhulidwe ka pa msewu, “Nsangalabwi yokha ya pa doko.”
Ndipo Mose ankadziwa kuti Mulungu anali atamutuma iye uko chifukwa cha izo.
Mulungu ali nawo amuna odzazidwa ndi Mzimu Woyera kuti azitsogolera Mkwatibwi Wake; kuwatsogolera iwo KU PAKUTI ATERO AMBUYE, MNENERI MTHENGA. Pakuti Uthenga ndi m’thenga ali wofanana. Imeneyo ndiyo njira ya Mulungu yosasintha yoperekedwa ya tsiku la lero, ndiponso nthawi zonse.
Chifukwa iwo anamvetsera kwa cholakwika. Pamene Mose, wotsimikizidwira ndi Mulungu, ndi mtsogoleri kuti awasonyeze iwo njira yaku Dziko Lolonjezedwa, ndipo iwo anali atabwera patali chotere bwinobwino, komano iwo sakanakhoza kupitirira limodzi naye.
Tsopano, okhulupirira akhoza kuwaona Iwo, koma osakhulupirira sangakhoze kuwawona Iwo akutsimikizidwira.
Osati kokha kuti inu munasankhidwa kuti mulandire Vumbulutso lalikulu la nthawi yotsiriza ili la lero, koma Mulungu, mwa njira ya matepi Ake a Chakudya chosungidwa, amalankhula pakati pa mizere kwa Mkwatibwi Wake wokoma wa pamtima.
Ndiye ngati inu muli mwana wamwamuna wa Mulungu kapena mwana wamkazi wa Mulungu, inu munali mwa Mulungu nthawiyonseyo. Koma Iye ankadziwa kama wake ndi nthawi yomwe inu mukanati mudzabzalidwe. Kotero tsopano inu mwapangidwa cholengedwa, mwana wamwamuna wa Mulungu, mwana wamwamuna kapena wamkazi wa Mulungu wowonetseredwa kuti mukomane ndi chitsutso cha ora lino kuti mutsimikizitsire Mulungu woona ndi wamoyo wa ora lino, Uthenga umene ukubwerapowu mu nthawi ino. Uko nkulondola! Inu munapangidwa uko asanakhazikitsidwe maziko a dziko.
Ndi kalata yachikondi bwanji yapakati pa mizere kwa Mkwatibwi Wake, ULEMERERO!!! Osati kokha kuti Iye anatidziwa ndi kutisankha ife asanaikidwe maziko a dziko, koma pano Iye akutiuza ife kuti Iye anatisankha ife kuti tikhale ana Ake aamuna ndi aakazi owonetseredwa a LERO. Iye anatiika ife pano pa dziko lapansi lero, pamwamba pa oyera mtima ena onse kuyambira pachiyambi, chifukwa Iye ankadziwa kuti ife tikanati tidzakumane ndi vuto la ora lino kuti titsimikizire Mulungu woona ndi wamoyo wa ora lino, Uthenga umene ukubwera mu nthawi ino.
Ife tinali mwa Mulungu, jini, mawu, chikhumbo kuchokera kuchiyambi, koma TSOPANO Ife tikukhala PAMODZI mu malo Ammwambamwamba mwa Khristu Yesu, kuyankhulana ndi Iye mwa Mawu Ake, kupyolera mu Mawu Ake; pakuti ife NDIFE MAWU AKE, ndipo Iwo akudyetsa miyoyo yathu.
Sitingathe, ndipo sitidzabayilamo kalikonse m’miyoyo yathu koma Mawu osaipitsidwa a Mulungu. Timazindikira ndikukhulupirira kuti ndi njira yoperekedwa ndi Mulungu ya lero.
Ife tikanakonda kuti inu mubwere kuzajowinana nafe Lamlungu lino pa 12:00 p.m., nthawi ya ku Jeffersonville, pamene ife tikumva LIWU LOKHA, Liwu la Mulungu pa matepi, inu mukhoza kunena kuti AMEN kwa Mawu aliwonse omwe inu mumawamva.
M’bale. Joseph Branham
Uthenga: Zochitika Zamakono Zimamveka Bwino Ndi Uneneri 65-1206
Malemba oti muwerenge musanamve Uthenga:
Genesis 22
Deuteronomo 18:15
Masalimo 16:10 / 22:1 / 22:18 / 22:7-8 / 35:11
Yesaya 7:14 / 9:6 / 35:7 / 50:6 / 53:9 / 53:12 / 40:3
Amosi 3:7
Zekariya 11:12; 13:7/14:7
Malaki 3:1/4:5-6
Mateyu woyera 4:4 / 24:24 / 11:1-19
Luka woyera 17:22-30 / 24:13–27
Ahebri 13:8; 1:1
Yohane Woyera 1:1
Chivumbulutso 3:14-21; 10:7