Uthenga: 62-1014E Namulondola
Okondedwa gulu la Mkwatibwi
Ndipo tsopano Mulungu nthawizonse wakhala akutumiza anamulondola Ake, Iye nthawizonse sanayambe wakhalapo wopanda namulondola, nthawizonse kudutsa mmibadwo. Mulungu nthawizonse amakhala naye wina amene amamuimirira Iye pa dziko lapansi ili, mu mibadwo yonse.
Mulungu safuna kuti tizidalira kumvetsa kwathu kapena maganizo opangidwa ndi anthu. Ndi chifukwa chake amatumiza Mkwatibwi Wake Mtsogoleri; pakuti ali ndi kunvetsa, pomuka ndi choti achite. Mulungu SANAYAMBE WASINTHAPO dongosolo Lake. Iye sanalepherepo kutumiza Namulondola kwa anthu Ake, koma inu muyenera kumuvomereza Namulondola ameneyo.
Inu muyenera kukhulupirira Mawu aliwonse amene Iye amanena kupyolera mwa Namulondola Wake. Iwe uyenera kupita momwe Namulondola Wake akuti uzipita. Ngati muyamba kumvetsera ndi kukhulupirira mawu ena monga kalozera wanu,inu mudzangotayika.
Yohane Woyera 16 akuti Iye anali ndi zinthu zambiri zoti atiuze ife ndi kutiululira kwa ife, potero Iye amatumiza Mzimu Wake Woyera kuti Utitsogolere ndi kutiuza ife. Iye anati Mzimu Woyera ndiye mneneri wotsogolera wa m’badwo uliwonse. Choncho, aneneri ake anatumidwa kuimira Mzimu Woyera kuti atsogolere Mkwatibwi Wake.
Mzimu Woyera umatumizidwa kuti udzatsogolere mpingo, osati gulu lina la amuna. Mzimu Woyera ndiwo luntha-lonse. Anthu amayamba kumakhuthala, amakhala osayanjanitsika.
Si munthuyo, koma Mzimu Woyera MWA munthu ameneyo. Munthu amene anamusankha kuti adziyimire yekha ndi kukhala mtsogoleri wathu wapadziko lapansi amene amatsogoleredwa ndi Mtsogoleri wathu wa Kumwamba. Mawu amatiuza ife kuti tiyenera kumutsatira Namulondola ameneyo. Ziribe kanthu zomwe timaganiza, zomwe zikuwoneka ngati zomveka, kapena zomwe munthu wina anganene, sitiyenera kugawa izi, wotsogolera ndi mmodzi yekha.
Mulungu amatumiza Namulondola, ndipo Mulungu amafuna kuti inu muzikumbukira kuti ameneyo ndi Namulondola Wake woikidwapo.
Mtsogoleri wathu mneneri wasankhidwa ndi Mulungu kuti alankhule Mawu Ake. Mawu ake NDI MAWU A MULUNGU. Mtsogoleri wa mneneri, ndipo iye yekha, ali nako kutanthauzira Kwauzimu kwa Mawu. Mulungu analankhula Mawu Ake kwa iye mulomo kwa khutu. Chifukwa chake, simungathe kutsutsa, kusintha, kapena kulingalira Mawu a Mtsogoleri wanu.
Inu muyenera kumutsatira Iye, ndipo Iye yekha. Ngati simutero, mudzatayika. Kumbukirani, pamene musiya Iye, Wotsogolera wosankhidwa ndi Mulungu, mumakhala nokha, kotero ife tikufuna kukhala pafupi ndi namulondola yemwe Iye anamusankha, ndi kumva ndi kumvera Mawu aliwonse amene Iye amanena kupyolera mwa iye.
Mtsogoleri wathu watiphunzitsa kuti chipangano chakale chinali mthunzi wa chipangano chatsopano.
Pamene Aisrayeli anachoka ku Igupto kupita ku dziko lolonjezedwa, pa Eksodo 13:21 , Mulungu anadziŵa kuti iwo anali asanayendepo mwanjira imeneyo. Anali ma mailosi makumi anayi okha, komabe iwo ankasowa chinachake choti apite nawo. Iwo anataya njira yawo. Kotero Iye, Mulungu, anawatumizira iwo Mtsogoleri. Eksodo 13:21, chinachake chonga chonchi, “Ine ndikutumiza Mngelo Wanga patsogolo panu, Lawi la Moto, kuti likusungeni inu panjira,” kuti likawalondolere iwo ku dziko lolonjezedwa ili. Ndipo ana a Israeli ankatsatira Namulondola uja, Lawi la Moto (usiku), Mtambo usana. Pamene Iwo anaima, iwo anaima. Pamene Iwo adayenda, adayenda. Ndipo pamene Iye anawafikitsa iwo kufupi ndi dziko, ndipo iwo sanali oyenera kuti awoloke, Iye anawatsogolera iwo kubwerera ku chipululu kachiwiri.
Iye anati umenewo ndi mpingo lero. Ife tikanapita kale tikadangodzikonza tokha ndi kukhala mu dongosolo, koma Iye anachita kutitsogolera ife kuzungulira ndi kuzungulira ndi kuzungulira.
Iwo anali oti angotsatira wotsogolera wawo pamene IYE AMATSATIRA ndi kumva kuchokera ku Lawi la Moto. Iye anawauza iwo zimene Mulungu ananena ndipo iwo anayenera kumvera Mawu aliwonse amene iye ananena. Iye anali Liwu la Namulondola. Koma anafunsa ndi kukangana ndi wotsogolera woikidwa ndi Mulungu, motero anayendayenda m’chipululu kwa zaka makumi anayi.
Panali atumiki ambiri m’masiku a Mose. Mulungu anawasankha kuti athandize anthu, monganso Mose sakanatha kuchita zonsezi. Koma udindo wawo unali kuwalozera anthu ku zimene Mose ananena. Baibulo silimanena chirichonse chimene amuna amenewo ananena, ilo limangoti zimene Mose ananena kuti ndi Mawu kuti azitsogolera anthu.
Pamene Mulungu anamuchotsa Mose pamalopo, Yoswa anadzozedwa kuti azitsogolera anthu, zomwe zikuimira Mzimu Woyera lero. Yoswa sanalalikire china chatsopano, komanso sanayese kutenga malo a Mose, komanso sanayese kutanthauzira zomwe wotsogolera ananena; iye anangowerenga zimene Mose ananena ndi kuwauza anthu, “Khalani ndi Mawu. Anangowerenga zimene Mose ananena.
Ndi mtundu wangwiro bwanji wa lero. Mulungu anamutsimikizira Mose ndi Lawi la Moto. Mneneri wathu anatsimikiziridwa ndi Lawi la Moto lomwelo. Mawu amene Mose analankhula anali Mawu a Mulungu ndipo anaikidwa mu Likasa.
Pamene Mose anachotsedwapo, Yoswa anadzozedwa kutsogolera anthu mwa kusunga Mawu amene Mose analankhula pamaso pawo. Iye anawauza iwo kuti akhulupirire ndi kukhala ndi Mawu aliwonse amene kalozera wa Mulungu analankhula.
Yoswa nthaŵi zonse ankaŵerenga zimene Mose analemba Mawu ndi Mawu m’mipukutu. Iye anayika Mawu pamaso pawo nthawizonse. Mawu a tsiku lathu sanalembedwe, koma Iwo anajambulidwa kotero kuti Mzimu Woyera ukhoze kukhala ndi Mkwatibwi Wake kumva Mawu pa Mawu chimene Iye analankhula, mwa Kukanikiza kusewera.
Mulungu sasintha dongosolo Lake. Iye ndi Namulondola wathu. Liwu Lake ndi lomwe likutsogolera ndi kugwirizanitsa Mkwatibwi Wake lero. Ife timangofuna kumva Liwu la Namulondola wathu pamene Ilo limatitsogolera ife ndi Lawi la Moto. Ndi chilumikizano chosaoneka ndi maso cha Mkwatibwi wa Khristu. Ife timalidziwa Liwu Lake.
Pamene namulondola wathu abwera pa guwa, Mzimu Woyera umamukhudza iye ndipo Iwo sulinso iye, koma Namulondola wathu. Iye akukweza mutu wake m’mwamba ndi kufuula, “Atero Ambuye, Atero Ambuye, Atero Ambuye! Ndipo membala aliyense wa Mkwatibwi wa Khristu kuzungulira dziko amabwera kumene kwa iye. Chifukwa chiyani? IFE TIMAMUDZIWA MTSOGOLERI WATHU MMENE IYE AMAYANKHULIRA.
Mtsogoleri Wathu = Mawu
Mawu = Amadza kwa mneneri
Mneneri = Mulungu womasulira yekha waumulungu; Mtsogoleri wake wapadziko lapansi.
58 Muzikhala kumbuyo kwa Mawu! O, inde, bwana! Muzikhala ndi Namulondola ameneyo. Muzikhala kumbuyo komwe kwa Iye. Musamapite kutsogolo kwa Iye, inu muzikhala kumbuyo kwa Iye. Muzimulola Iye kuti azikutsogolerani inu, osati inu muzimutsogolera Iye. Inu muzimulola Iye kuti azipita.
Ngati inu simukufuna kuti mutayike, bwerani mudzamvetsere kwa Namulondola wathu pamene Iye akuyankhula kupyolera mu kalozera Wake woikidwa pa dziko Lamlungu lino pa 12:00 p.M., nthawi ya ku Jeffersonville.
M’bale. Joseph Branham
Uthenga:
62-1014E – Namulondola
Malemba:
Marko 16:15-18
Yohane 1:1/16:7-15
Machitidwe 2:38
Aefeso 4:11-13; 4:30
Ahebri 4:12
2 Petulo 1:21
Eksodo 13:21