Uthenga: 63-0322 Chisindikizo Chachisanu
- 25-0413 Chisindikizo Chachisanu
- 23-0820 Chisindikizo Chachisanu
- 22-0227 Chisindikizo Chachisanu
- 21-0221 Chisindikizo Chachisanu
- 19-0504 Chisindikizo Chachisanu
- 17-0408 Chisindikizo Chachisanu
Okondedwa Iwo Akupumula,
Ife tiri pano. Ife Tafika. Kutsimikizira kwa Mawu kwatsimikizira kuti Vumbulutso lathu la Uthenga uwu likuchokera kwa Mulungu. Ife tiri mu CHIFUNIRO Chake CHANGWIRO pakukhala ndi Liwu la Mulungu pa matepi.
Kodi KUKANIKIZA KUSEWERA ndikofunika bwanji? Mawu omwe tikuwamva pa matepi ndi ofunikira kwambiri, opatulika kwambiri, mwakuti Mulungu Mwiniwake sakanawadalira Iwo ngakhale kwa Mngelo…osati ngakhale kwa mmodzi wa Angelo Ake a Kumwamba. Izo zinkayenera kuti ziwululidwe ndi kubweretsedwa kwa Mkwatibwi Wake ndi mneneri Wake, chifukwa ndi amene Mawu a Mulungu amadzako, mneneri Wake, YEKHA.
Mulungu anadulapo Zisindikizo, analipereka Ilo kwa mtumiki Wake wa mngelo wachisanu ndi chiwiri, ndipo anawulula Bukhu lonse la Chivumbulutso kwa iye. Kenako, Mulungu analankhula kudzera mwa mngelo Wake wapadziko lapansi ndipo anaulula ZONSE kwa Mkwatibwi Wake.
Kanthu kakang’ono kalikonse mwatsatanetsatane kalankhulidwa ndikuwululidwa kwa ife. Mulungu adatisamala ife kwambiri moti sanangotiuza zimene zakhala zikuchitika pano padziko lapansi kuchokera pachiyambi cha nthawi komanso analankhula kudzera mwa mngelo wake ndi kutiuza ife za zimene zikuchitika pano m’malo ngati paradaiso pakali panopa.
Sanafune kuti tizidera nkhawa, kapena kuti tisakayikire zimene zidzatichitikire tikadzachoka m’chihema chimenechi. Kotero, Mulungu Mwiniwake anamutengera mngelo Wake wamphamvu wachisanu ndi chiwiri kudutsa katani la nthawi, kotero kuti iye akakhoze kuchiwona Icho, kuchimverera Icho, ngakhale kuyankhula kwa iwo Kumeneko. Sanali masomphenya, iye anali UKO.
Mulungu anamutengera kumeneko kuti abwerere nadzatiuza kuti: “Ndinali kumeneko, ndinaziwona Izo. Zikuchitika TSOPANO…Amayi athu, atate athu, abale athu, alongo athu, ana aamuna, ana aakazi, akazi, amuna, agogo, Mose, Eliya, WOYERA ONSE amene anatsogola kale ali kumeneko atavala Zovala Zoyera, akupumula ndi kutiyembekezera ife”.
Ife sitidzaliranso, chifukwa Icho chidzakhala chimwemwe chokhachokha. Sitidzakhalanso achisoni, chifukwa Icho chidzakhala chisangalalo chokhachokha. Ife sitidzafa konse, chifukwa Iwo ndi moyo wosatha. Sitingathe kukalamba, chifukwa tonse tidzakhala achichepere kwamuyaya.
Ndi ungwiro…kuphatikizapo ungwiro…kuphatikizaponso ungwiro, ndipo ife tikupita kumeneko!! Ndipo monga Mose, sitisiya ngakhale chiboda,IFE TONSE TIKUPITA… BANJA LATHU LONSE.
Kodi kuli kofunika bwanji KUKONDA m’ngelo wamphamvu wachisanu ndi chiwiriyo?
Ndipo Ilo linafuula, linati, “Zonse zomwe inu munazikondapo…” mphotho ya utumiki wanga. Ine sindikusowa mphotho. Iye anati, “Zonse zimene inu munazikondapo konse, ndi zonse zomwe zinayamba zakukondani inu, Mulungu wazipereka kwa inu.”
Tiyeni tiwerengenso chonde: Kodi Iye anati chiyani?….Mulungu wakupatsani INU!!
Ndipo tidzalowa nawo limodzi ndikukuwa, “Tikupumula“
Kodi kopita kwathu kwamuyaya tikupumulira pa chiyani? MAWU ALIWONSE AMENE ANALANKHULIDWA PA MATEPI. Ndine wothokoza kwambiri kwa Ambuye kuti watipatsa Vumbulutso Loona kuti kumakanikiza kusewera ndichinthu CHOFUNIKA KWAMBIRI chomwe Mkwatibwi ayenera kuchita.
Kodi mungafune kupumula nafe? Bwerani mudzalumikizane nafe Lamlungu lino nthawi ya 12:00 P.M., nthawi ya ku Jeffersonville, pamene tikumva zonse za tsogolo, komwe tikupita, ndi momwe tingakafikire kumeneko, pamene tikumva Liwu la Mulungu likulankhula ndi kutsegula: Chisindikizo Chachisanu 63-0322.
M’bale. Joseph Branham
Malemba oti muwerenge musanamve Uthenga:
Danieli 9:20-27 Machitidwe 15:13-14 Aroma 11:25-26 Chivumbulutso 6:9-11 / 11:7-8 / 22:8-9