25-0330 Chisindikizo Chachitatu

Uthenga: 63-0320 Chisindikizo Chachitatu

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Eva Wauzimu,

Ndiroleni ine ndiyambe kalata yanga lero ndi bomba la atomiki la Mulungu; osati mfuti ya zipolopolo makumi awiri ndi ziwiri kwa Mkwatibwi wa Yesu Khristu.

Tsopano, ngati inu mukufuna kuzilemba izo; Inde, inu nonse mumawadziwa: Yesu, Yohane 14:12; ndi Yoweli, Yoweli 2:38; Paulo, Timoteo Wachiwiri 3; Malaki, mutu wa 4; ndi Yohane mvumbulutsi , Chivumbulutso 10:17, 1-17 . Mwaona, ndendende zomwe zikanati zidzachitike tsopano!

Chidziwitso ndi chenjezo: Mawu otsatirawa si anu ngati mumakhulupirira.

“Ife timayika kwambiri pa mneneri wa Mulungu.” “Iwe sungakhale Mkwatibwi ngati iwe ungomvetsera kwa mneneri.” “Kusewera matepi mu mpingo ndi kulakwa.” “Tochi yadutsidwa; chofunika kwambiri masiku ano ndikumvetsera ulaliki.” “Kuyikanikiza kusewera zonse pa nthawi imodzi ndi chipembedzo.”

Kwa mpingo, ndi chiyani Icho? Mawu mu thupi anapangidwa thupi pakati pa anthu Ake kachiwiri! Mwaona?

Bumu…Choncho poyikanikiza kusewera, titha kumva Mawu obadwa thupi akusandulika thupi, akulankhula kuchokera ku mlomo kupita ku khutu kwa ife pamene Iye akuwulula Mawu Ake.

Ndipo wina anganene kuti si MAWU OFUNIKA KWAMBIRI KUWAMVA? Gawo ili la mawuwo ndi lanu.

Ndipo iwo sakhulupirira Izo basi.

Pamene vumbulutso lochuluka limene Ambuye amatipatsa ife la Mawu Ake, ndi chimene ife tiri, ndipamenenso aliyense kunja kwa vumbulutso limenero amafikira kutali.

Ndiroleni ine ndinene icho, kwenikweni, kotero inu mudza…icho chidzalowerera mpaka pansi. Ine ndikufuna ichi kuti mumvetse icho. Ndilo liri vuto ndi inu lero, onani, inu simukuwadziwa Mawu! Mwawona?

Mulungu ali ndi amuna odzozedwa kuti azilalikira Uthenga uwu, koma pali Mtheradi umodzi wokha: Mawu. Pamene mumva mtumiki, kapena wina aliyense akulankhula, muyenera kukhala ndi chikhulupiriro kuti mukhulupirire kuti zimene akunena ndi NDENDENDE zomwe Mneneri wa Mulungu ananena kale. Mawu awo, vumbulutso lawo, kutanthauzira kwawo kukhoza kulephera; Liwu la Mulungu pa matepi SILINGALEPHERE KONSE.

Kuyankhula za Mulungu mu kuphweka ndikukanikiza kusewera…Akunenanso izo mobwereza.

Iwo amamuphonya Iye, Mawu amoyo owonetseredwa mu thupi, mwa Mawu amene alonjezedwa. Mawu analonjeza kuchita zinthu izi. Lonjezo linapangidwa, kuti izo zidzakhala monga chonchi mu masiku otsiriza.

Mvetserani ku Bingu Lake. Bingu ndi Liwu la Mulungu. William Marrion Branham ndi Liwu la Mulungu kwa m’badwo uno.

M—Mkwatibwi sanakhalebe nacho chitsitsimutso. Mwawona? Pakhala palibe chitsitsimutso pamenepo, palibe mawonetsedwe a Mulungu kuti amukondoweze Mkwatibwi panobe. Mwawona? Ife tikuyang’anira chimenecho tsopano. Zidzatengera mabingu asanu ndi awiri awo osadziwika kumbuyo uko, kuti amudzutse Iye kachiwiri, onani. Eya. Iye adzachitumiza icho. Iye analonjeza icho. Tsopano yang’anani.

Inu mukhoza kuzipotoza izo ngati mukufuna, koma Mabingu Asanu ndi awiri adzapatsa Mkwatibwi kukondoweza mwa Vumbulutso ndi chikhulupiriro chokwatulitsa, chimene chimadza kokha mwa Mzimu Woyera kuyankhula kupyolera mwa mneneri wa Mulungu. Zikuchitika TSOPANO padziko lonse lapansi. Mulungu ali ndi Mkwatibwi Wake Wokondowezedwa ndi Mawu Ake.

Osati zokhazo, koma Iye wamuwuza kale mdani wathu choti achite.

Iwe uchotse manja ako pa iwo. Iwo akudziwa kumene iwo akupita, pakuti iwo adzozedwa nawo Mafuta Anga. Ndipo pakukhala odzozedwa nawo Mafuta Anga, iwo ali naye vinyo wa chisangalalo, chifukwa iwo akudziwa Mawu Anga a lonjezo, ‘Ine ndidzawawukitsa iwo kachiwiri.’ Usati upweteke Izo! Usati upite kukayesa kuwasokoneza iwo.

Iye Wauza mdani wathu kuti achotse manja ake oipa pa ife. Koma kodi matenda angativutitsebe? Inde. Kodi tidakali ndi mavuto? Inde. Koma Iye anatiuzanso zoyenera kuchita.

Ndi zakuya. Werengani pang’onopang’ono ndi mobwerezabwereza.

Asanakhale Mawu, ali ganizo. Ndipo ganizo liyenera kulengedwa. Chabwino. Kotero, maganizo a Mulungu anakhala chirengedwe pamene iwo analankhulidwa, mwa mawu. Ndipo pamene Iye apereka iwo kwa—kwa inu ngati ganizo, ganizo Lake, ndipo ilo lawululidwa kwa inu. Ndiye, likadali ganizo mpaka inu mutalankhula ilo.

Malingaliro ake anakhala chilengedwa pamene icho chinalankhulidwa. Ndiye, maganizo Ake anaperekedwa ndi kuvumbulutsidwa kwa ife monga Mawu. Tsopano Ilo likadali ganizo ndi ife mpaka ife titayankhula Ilo. CHONCHO IFE TIMALANKHULA… NDIKUZIKHULUPIRIRA IZO.

Ine ndine Mbewu Yachifumu ya Abrahamu. Ine ndine Mkwatibwi wa Khristu. Ine ndinasankhidwa ndi kukonzedweratu asanaikidwe maziko a dziko kuti ndikhale Mkwatibwi Wake, ndipo palibe chimene chingasinthe zimenezo. Lonjezo lirilonse la m’Baibulo ndi langa. Ndi Mawu Ake kwa ine. Ndine wolowa wa Lonjezo lomwelo. Iye ndiye Ambuye Mulungu amene amachiritsa nthenda zanga zonse. Chirichonse chimene ine ndikufuna ndi changa, Mulungu ananena chomwecho.

Mulungu mu Kuphweka: Chikhulupiriro chimadza pakumva, kumvera Mawu. Mawu amadza kwa mneneri.

Aliyense akufuna kugwiritsa ntchito “ZOBWEREZA” kutsimikizira malingaliro awo, maganizo awo, uthenga wawo. Ndipo iwo akulondola, chomwechonso ine, ndi chifukwa chake zonse zomwe ine ndikukupatsani inu ndi mawu obwereza kuti ndikuuzeni inu: Khalani nawo Matepi. Mvetserani kwa Liwu limenelo. Liwu limenelo ndi Liwu la Mulungu. Inu muyenera kukhulupirira Mawu aliwonse pa Matepi, osati zomwe wina aliyense anena. Liwu Limenelo NDI MAWU OFUNIKA KWAMBIRI OMWE MUYENERA KUMVA.

Ena amagwiritsa ntchito mawu obwereza kuti akubweretseni inu ku utumiki wawo, ku mpingo wawo, kutanthauzira kwawo, vumbulutso lawo. “Khalani ndi abusa anu.” (Chabwino, ine ndimazikonda izo nanenso, chifukwa ife timachitaso izo, abusa osiyana basi.) “Iye si nsangalabwi yokhayo pa gombelo.” “Iye sananene ku kusewera matepi mu tchalitchi.”

Musati muyike kumasulira kwamtseri kulikonse kwa Iwo. Iye akufuna angwiro, osakhudzidwa, osati ngakhale kudzivula. Ine sindingafune mkazi wanga kumavulira amuna ena. Ndipo pamene inu mupita kukamvera ku malingaliro ena aliwonse, opyola Iwo, inu mukumvetsera, inu mukumuvulira Satana. Ameni! Kodi izo sizikukupangani inu kumverera mwachipembedzo? Mulungu akufuna inu mukhale osakhudzidwa. Mukhale pomwepo nawo Mawu amenewo. Mukhale pomwepo nawo Iwo. Chabwino.

Koma ine ndi nyumba yanga, Ife tidzakhala okanikiza kusewera ndi kutsatira Mawu Obadwa M’thupi a Mulungu akulankhula kudzera mwa mngelo Wake wachisanu ndi chiwiri. Ife sitidzawonjezera kutanthauzira kwathu kwamseri kwa Iwo; sitidzavulira kapena kumvera malingaliro aliwonse. Ife TIDZAKHALA NDI MAWU AMENEWO MONGA MOMWE ANALANKHULIDWILA PA MATEPI. Iwo Ndi Mulungu mu Kuphweka.

Ndi nthawi yaulemerero bwanji yomwe ife titi tidzakhale nayo Lamlungu lino pa 12:00 p.m., nthawi yaku Jeffersonville, pomwe ife tikumva: Chisindikizo Chachitatu 63-0320. Ndikufuna kukuitanani Inu kuti mubwere kuzalumikizana ndi ife pamene ife tikulumikizana mozungulira pa Mawu a tsiku la lero.

M’bale. Joseph Branham

Malemba oti Muwerenge musanayambe kumvera Uthenga:
Mateyu woyera 25:3-4
Yohane woyera 1:1, 1:14, 14:12, 17:17
Machitidwe Mutu Wachiwiri
Timoteyo woyamba 3:16
Ahebri 4:12, 13:8
Yohane woyamba 5:7
Levitiko 8:12
Yeremiya mutu wa 32
Yoweli 2:28
Zekariya 4:12

Ndiloleni nditengere mwayi uwu kuti ndifotokozenso ichi momveka bwino mobwereza. Ine sindikutsutsana ndi utumiki wofutukuka usanu. Ine ndimakhulupirira mu utumiki wofutukuka usanu. Sindikuona kuti n’kulakwa kumvera mtumiki. Ndikukhulupirira kuti muyenera kumvera abusa anu kumene Mulungu wakuyikani. Mfundo yanga ndi iyi yakuti, ndikukhulupirira kuti Mulungu anatumiza mneneri m’tsiku lathu. Mulungu anaulula Mawu Ake kwa mneneri Wake. Ine ndikhoza kulakwitsa, abusa anu akhoza kulakwitsa, koma ife TIYENERA kuvomereza (ngati ife timanena kuti ife tikukhulupirira UTHENGA UWU kuti ndi Choonadi ndipo M’bale Branham ndi mneneri wa Mulungu) zimene zikunenedwa pa matepi ndi PAKUTI ATERO AMBUYE. Ngati inu simukukhulupirira izo, ndiye inu simukukhulupirira Uthenga uwu. Chifukwa chake, ndikukhulupirira kuti ndi MAWU OFUNIKA KWAMBIRI AMENE MUYENERA KUMVA. Inu simukusowa kuti muzindimva ine, inu simusowa kuti mumve wina aliyense, koma INU MUYENERA KUMVA MAWU AMENE ALI PA TEPI.