25-0316 Chisindikizo Choyamba

Uthenga: 63-0318 Chisindikizo Choyamba

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa Wanga Mfumukazi ya Kumwamba,

Ine Ndili nazo zochuruka za inu munkhokwe Lamlungu lino. Choyamba, mudzamva kugunda kwa Bingu.  Ilo lidzakhala Liwu Langa, Liwu la Mulungu kuyankhula kwa inu, Mkwatibwi Wanga. Ndidzakhala ndikuwululira Mawu Anga kwa inu kuposa kale. Inu mudzandiwona Ine, Mwanawankhosa wamagazi amene anaphedwa kuchokera ku maziko a dziko, akutenga ndi kutsegula Bukhu, kumatula Zisindikizo, ndi kulitumiza Ilo kumusi uko ku dziko lapansi, kwa m’thenga Wanga wa mngelo wachisanu ndi chiwiri, William Marrion Branham, kuti adzawululire kwa INU zinsinsi zimene zakhala ziri zobisika kuchokera ku maziko a dziko!

Kudzakhala kukuwa, kufuula, ndi ma aleluya ochokera kuzungulira dziko lonse pamene ine ndikuyankhula kwa inu. Mkango udzakhala ukubangula; odzozedwa, mphamvu, ulemerero, mawonetseredwe adzakhala oposera mawu. Inu, Mfumukazi Yanga, mudzakhala pamodzi m’malo amwambamwamba pamene Ine ndikulankhula ndi inu ndi kukupatsani inu mphavu ya Chikhulupiriro yokwatulitsa. Ife

Kumbukirani, inu muyenera kukhala nacho Chikhulupiriro chija chimene chinaperekedwa kamodzi kwa oyera. Ndinakuuzani kuti, Muzimvera mngelo wanga amene ndinamutuma kwa inu.

Iye ali woti “abwezeretse Chikhulupiriro cha ana kubwerera kwa atate.” Chikhulupiriro choyambirira cha Baibulo ndi chakuti chibwezeretsedwe ndi mngelo wachisanu ndi chiwiri.

Mawu Anga amakuuzani inu, mu masiku a Liwu la mngelo wachisanu ndi chiwiri, kuwomba kwake, kuwomba lipenga la Uthenga; ayenera kutsiriza zinsinsi zonse za Mulungu. Sipangakhoze kukhala chinthu chimodzi chowonjezedwako ndipo palibe chochotsedwapo kwa chimene ine ndinanena pa matepi; muzingonena zomwe ndidalankhula kudzera mwa m’thenga Wanga wa m’ngelo. Ichi ndichifukwa chake ndinali nalo ilo lidajambulidwa, kuti mophweka muzingotha ​​KUSINDIKIZA KULISEWERA ndikumva ndendende zomwe ndinanena, ndi momwe Ine ndinazinenera. Idzakupatsani Inu mphavu ya Chikhulupiriro chokwatulitsa.

Mfumukazi yanga yokondedwa, m’maso mwanga inu muli wangwiro, mtheradi, wopanda uchimo pamaso panga. Osadandaula, Inu SIMUDZAPITA mu chisautso; pakuti mwalandira Magazi Anga, Mawu Anga, mngelo Wanga, Liwu Langa, kotero inu kwenikweni mulibe uchimo pamaso panga.

Ine Ndilinazo Izo zainu zazikulu munkhokwe. Inu mukuwona Mawu Anga akufutukuka pamaso panu tsiku lililonse. Ndakhala ndikuyika zizindikiro kumwamba kuti ndikuuzeni kuti chinachake chikukonzekera kuchitika. Ine Ndikubwera, khalani okonzekera. Ikani Mawu Anga, Liwu Langa, choyamba m’moyo wanu.

Ikani chirichonse pambali, palibe chinthu chofunika kwambiri kuposa Mawu Anga. Ndikudziwa kuti m’dani akufuna kukugwetsani, koma ndinakulonjezani kuti ndidzakukwezani. Ine ndiri ndi inu, ngakhale MWA INU. Inu ndi Ine tikukhala Amodzi pamene Ine ndikuwululira Mawu Anga kwa inu.
Inu mukudziwa mu mtima mwanu, NDINU Mfumukazi Mkwatibwi wanga. Inu mukudziwa ine ndinakukonzeranitu inu. MUkudziwa kuti ndimakukondani. Mukudziwa kuti ndimakhala nanu mphindi iliyonse ya tsiku lililonse. Inu mukudziwa kuti Ine SINDIDZAKUSIYANI INU.

Tizikhala ndi nthawi yodabwitsa yotere pamene ndikukuwululirani zambiri Lamlungu lililonse, tsiku lililonse, pamene mukundimva Ine ndikulankhula kudzera mwa mngelo Wanga kwa inu. Ena mwina sangamvetse kapena kuwona zomwe inu mukuwona, koma Izo zazikika mu mtima mwanu kuti iyi ndi Njira Yanga yoperekedwa.

Ndi pothawirapo bwanji ndakupatsani inu. Inu mophweka Mutha Kungosindikiza kuSewera nthawi ina iliyonse, masana kapena usiku, ndikundimva ine Ndikulankhula nanu. Ndidzabweretsa chitonthozo ku moyo wanu pamene ndikuwululira Mawu Anga ndikukuuzani inu yemwe inu muli. Uthenga uliwonse ndi wa Inu, ndipo wa inu nokha. Tikhoza kuyanjana ndi kupembedza limodzi nthawi iliyonse yomwe inu mukufuna.

Lamlungu pa 12:00 P.M., nthawi ya ku Jeffersonville, gawo la Mkwatibwi lidzasonkhanitsidwa kuchokera kuzungulira dziko kuti adzamve zinsinsi zazikulu izi zikuwululidwa. Ine Ndikukuitanani inu kuti mubwere kulumikizana nafe pomwe tikumvera, 63-0318 – “Chisindikizo Choyamba”.

M’bale. Joseph

Malemba oti muwerenge pokonzekera kumva Uthenga:
Mateyu 10:1 / 11:1-14 / 24:6 / 28:19
Yohane 12:23-28
Machitidwe 2:38
2 Atesalonika 2:3-12
Ahebri 4:12
Chivumbulutso 6:1-2 / 10:1-7 / 12:7-9 / 13:16 / 19:11-16
Malaki chaputala chachitatu ndi chaputala cha folo
Daniele 8:23-25/11:21/9:25-27