25-0309 Cholekanitsa Pakati Pa Mibadwo Isanu Ndi Iwiri Ya Mpingo Ndi Zisindikizo Zisanu Ndi Ziwiri

Uthenga: 63-0317E Cholekanitsa Pakati Pa Mibadwo Isanu Ndi Iwiri Ya Mpingo Ndi Zisindikizo Zisanu Ndi Ziwiri

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa Iwo Obwezeretsedwa,

Ine Sinditopa kumva Liwu la Mulungu likutiuza kuti ndife ndani, komwe timachokera, komwe tikupita, zomwe tili.
wolandira cholowa, ndi momwe amatikondera ife.

unsembe wauzimu, fuko lachifumu, kupereka nsembe zauzimu kwa Mulungu, zipatso za milomo yawo, kupereka mayamiko kwa Dzina Lake.” Ndi a—ndi anthu otani! Iye ali nawo iwo.

Chitonthozo chathu chokha ndi mtendere zimadza pakumva Liwu la Mulungu likulankhula kwa ife, ndiye kulankhula mobwezera kwa Atate mwa kupereka nsembe zauzimu mwa zipatso za milomo yathu, kupereka matamando ku Dzina Lake.

Dziko lonseli likubuula. Chirengedwe chikubuula. Ife tikubuula ndi kuyembekezera kudza kwa Ambuye. Dzikoli lilibe kanthu kwa ife. Ife tiri okonzeka kuti tichoke ndi kupita ku Mgonero wathu wa Chikwati ndi Kwathu Kwamtsogolo limodzi ndi Iye ndi onse amene ali Kumeneko, basi kupyola katani ya nthawi, akutiyembekezera ife.

Tiyeni tidzuke tidzigwedeze tokha! Tsinani chikumbumtima chathu, tidzidzutse tokha ku zomwe zikuchitika pakali pano ndi zomwe zidzachitike mu mphindi ya kuphethira kwa diso.

Palibe mu mbiriyakale ya dziko zomwe zakhala zotheka kuti Mkwatibwi wa Khristu akhale wolumikizana kuchokera kuzungulira dziko, onse pa nthawi yofanana yomweyo, kuti amve Liwu la Mulungu likuyankhula ndi kuwulula Mawu Ake kwa Mkwatibwi Wake.

Okhulupirira, dzifunseni nokha, ndi liwu liti, mtumiki wuti, munthu uti, angalumikizitse ndi kubweretsa Mkwatibwi wa Khristu pamodzi? Ngati inu muli Mkwatibwi wa Khristu, inu mukudziwa kuti palibenso Liwu lina koma Liwu la Mulungu pa matepi.

Inde, Mzimu Woyera uli mwa aliyense wa ife, mu udindo uliwonse wa mpingo, koma Mulungu Mwiniwake anatiuza ife kuti Iye adzaweruza dziko ndi Mawu Ake. Mkwatibwi amadziwa kuti Mawu Ake amabwera kwa mneneri Wake. Mneneri wake ndi YEKHAYO wotanthauzira Wauzimu wa Mawu Ake. Zimene Iye analankhula sizingawonjezedwepo kapena kuchotsedwapo. Ndi Mawu,a pa matepi, amene ife tonse tidzaweruzidwa nawo, ndipo palibe mawu ena kapena kutanthauzira kwa Mawu amenewo.

Sizingatheke kuti liwu lina lirilonse ligwirizanitse Mkwatibwi. Ndi Liwu la Mulungu lokha pa matepi lingakhoze kugwirizanitsa Mkwatibwi Wake. Ndi Mawu okhawo omwe Mkwatibwi angagwirizane nawo. Ndi Liwu lokhalo limene Mulungu Mwiniwake anatsimikizira kukhala Liwu Lake kwa Mkwatibwi Wake. Mkwatibwi Wake ayenera kukhala mu Malingaliro Amodzi ndi Chigwirizano Chimodzi kuti akhale ndi Iye.

Ma tumiki akhoza kutumikira, aphunzitsi akhoza kuphunzitsa, azibusa akhoza kuchitira ubusa, koma Liwu la Mulungu pa matepi liyenera kukhala Liwu lofunika kwambiri lomwe iwo ayenera kuliyika pamaso pa anthu. Iwo ndiwo Mtheradi wa Mkwatibwi.

Ngati muli ndi Vumbulutso la izo, ndiye ichi ndi chimene chiti chichitike.

Mawu amatiuza ife kuti Adamu anataya cholowa chake, dziko lapansi. Tsopano, ilo linachoka mdzanja lake kupita kwa iye amene anamugulitsa, Satana. Iye anagulitsa chikhulupiriro chake mwa Mulungu, kwa malingaliro a Satana. ndipo iye analanditsa chidutswa chirichonse kwa manja a Satana. Iye anachipereka icho kuchokera mdzanja lake kupita kwa Satana.

Mulungu ndi Mulungu wa chilengedwe chonse, kulikonse, koma Mwana Wake, Adamu, anali ndi dziko lapansi ili pansi pa ulamuliro wake. Iye amakhoza kuyankhula, iye amakhoza kutcha dzina, iye amakhoza kunena, iye amakhoza kuimitsa chirengedwe, iye ankakhoza kuchita chirichonse chimene iye ankafuna kutero. Iye anali ndi ulamuliro wathunthu, wapamwamba kwambiri padziko lapansi.

Adamu anataya zonse, koma ulemerero kwa Mulungu, zonse zomwe iye anataya ndi kulandidwa zidawomboledwa ndi Muomboli wathu Wachibale, palibe wina koma Mulungu Wamphamvuzonse, amene anakhala Emanuele, mmodzi wa ife. TSOPANO, NDI ZATHU.

Ndife ana Ake aamuna ndi aakazi amene ati adzalamulire ndi kukhala mafumu ndi ansembe limodzi ndi Iye. Tili ndi moyo wosatha ndi Iye ndi onse amene timawakonda. Sipadzakhalanso matenda, sipadzakhalanso chisoni, sipadzakhalanso imfa, umuyaya basi zonse palimodzi.

Tikaganizira zimenezi, tingalole bwanji kuti mdierekezi atigwetse pansi? Ndi ATHU, ndikomwe tikupita posachedwa. Iye watipatsa ife chinthu chachikulu kwambiri chimene angatipatse ife. Masiku ochepa awa a mayeso ndi mayesero padziko lapansi amizidwa mwachangu ndi KUGONJETSA KWATHU KWAKUKULU MASIKU CHABE OMWE ALI PA TSOGOLO PATHU.

CHIKHULUPIRIRO chathu sichinakhale chokulirapo. Chisangalalo chathu sichinakhalepo chachikulu. Timadziwa kuti ndife ndani komanso komwe tikupita. Tikudziwa kuti tili mu chifuniro Chake changwiro pa kukhala ndi Mawu Ake. Chomwe ife tikusowa kuti tichite ndi kukhala nawo matepi ndi kukhulupirira Mawu aliwonse; osati kuvetsa zonse, KOMA KUKHULUPILIRA MAWU ONSE…ndipo TIMAWACHITA!

Chikhulupiriro chimadza pakumva, kumva Mawu. Mawu amadza kwa mneneri. Mulungu analankhula Izo. Mulungu anazijambula Izo. Mulungu anaulula Izo. Ife tikuzimva Izo. Ife timakhulupirira IZO.

Inu mukhoza kupeza Vumbulutso ili kokha pa kumva Liwu la Mulungu pa matepi.

Zonse izo zimene Khristu ati adzachite pa matsiriziro zidzaululidwa kwa ife sabata ino, mu Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri, ngati Mulungu angatilole ife. Mwaona? Chabwino. Izo zidzaululidwa. Ndi kuululidwa, pamene Zisindikizo zikutsegulidwa ndi kuperekedwa kwa ife, ndiye ife tikhoza kuona chimene dongosolo lopambana la chiombolo ili liri, ndipo liti ndi momwe chiti chidzachitike. Zonsezo ndi zobisika mu Bukhu ili la chinsinsi pano. Ndi losindikizidwa, liri ndi Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri, ndipo kotero Mwanawankhosa ndi yekhayo Mmodzi Amene angamatule izo.

Lamlungu lino pa 12:00 P.M., nthawi yaku Jeffersonville, gawo la Mkwatibwi kuchokera kuzungulira dziko lapansi adzakhala akumvetsera ku Liwu la Mulungu onse pa nthawi imodzi. Tidzakhala tikugunda mwamphavu kumwamba ndi mapemphero athu ndi kumulambira IYE. Ndikukuitanani Inu kuti mubwere kulumikizana nafe pamene tikumva: Cholekanitsa Pakati Pa Mibadwo Isanu Ndi lwiri Ya Mpingo Ndi Zisindikizo Zisanu Ndi Ziwiri 63-0317E.

Chonde musaiwale za kusintha kwa nthawi yaku Jeffersonville kumapeto a sabata ino.

M’bale. Joseph Branham