25-0223 Kodi Ichi Ndi Chizindikiro Cha Mapeto, Bwana?

Uthenga: 62-1230E Kodi Ichi Ndi Chizindikiro Cha Mapeto, Bwana?

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa Mabwana,

Ichi ndi Chizindikiro. Iyi ndi nthawi. Uwu ndi, Uthenga. Awa ndi Mawu. Ili ndilo, Liwu la Mulungu. Uyu ndi Mwana wa Munthu. Iyi ndiyo, njira yoperekedwa ndi Mulungu. Awa ndiwo mapeto a nthawi.

Palibe m’neneri, palibe mtumwi, palibe, mu nthawi iliyonse, anayamba wakhalapo mu nthawi yotero yomwe ife tikukhalamo tsopano. Zalembedwa m’miyamba. Zalembedwa pa nkhope ya dziko lapansi. Zalembedwa m’nyuzipepala iliyonse. Awa ndiwo mapeto, ngati mungathe kuwerenga zolembedwa.

Iye amene ali nalo khutu, muloleni iye amve zomwe Mulungu anayankhula, ndi kuchita rekodi, kotero iwo sakanakhala mawu anga, maganizo anga, lingaliro langa, koma Liwu lomwe la Mulungu likulangiza Mkwatibwi Wake chimene chiri njira Yake YOKHA yangwiro yoperekedwa kwa lero.

Bwerani ndi kumvetsera pamene Iye akutiuza ndi kuwulula kwa ife mwa malembo, mwa masomphenya, mwa kutanthauzira kwa maloto, kuti tikhale ndi Uthenga, kuti tikhale ndi matepi. Muzinena ZOKHAZO zomwe zili pa matepi.

Palibe njira yabwino, kapena njira yotsimikizika, yoposa kumva Liwu la Mulungu kuchokera kwa Mulungu Mwiniwake. Mulungu analamulira Mkwatibwi Wake polankhula kupyolera mwa mneneri Wake ndi kutiuza ife, KUSINDIKIZA KUSEWERA, munyengo.

Lankhulani Ilo, lilalikireni ilo, chitirani umboni za ilo, ndi kuliwuza dziko lapansi za ilo, koma Iye amatiuza ife kuti pali njira imodzi yokha yangwiro yoperekedwa kuti afikitse Mkwatibwi ungwiro: kumvetsera kwa Liwu la Mulungu pa matepi. Ngati chinachake chikukudodometsani inu, sewerani tepiyo. Iyenera kukhala YOYAMBA, ndipo ndilo Liwu lofunika kwambiri lomwe muyenera kulimva. Ndi Mawu Ake angwiro amene anawayika pa tepi.

Tsopano fanizirani ngakhale ilo ndi enawo, maloto. Awa anali masomphenya. Chakudya, ndi Ichi apa. Awa ndiwo malowo.

Mvetserani, mwa maloto ndi masomphenya, Chakudya cha Mkwatibwi chiri kuti? Malowo ali kuti? Uthenga wa Mkwatibwi uli pa matepi.

Ndipo pano ndimamverera ngati kwathu, kwa ine. Malo ake ndi ano. Ndipo ngati inu mungazindikire, maloto anayankhula chinthu chomwecho, onani, kumene Chakudya.

Kuti atsimikizire kuti ife tiri nacho Icho, iye akutiuza ife kamodzinso, matepiwo ali Chakudya cha Mkwatibwi.

“Palibenso nthawi.” Ngati iyo ili, tiyeni tidzikonzekere tokha, abwenzi, kukakomana naye Mulungu wathu.

Inde, Ambuye, ndicho chokhumba cha mtima wathu, kukonzekera kukumana nanu, kuti ife tikhale Mkwatibwi Wanu. Tichite chiyani Ife Ambuye? Njira Yanu yoperekedwa ndi yotani? Dongolo lanu ndilotani? Njira Yanu yangwiro ndi iti? Inu munatitumizira ife mneneri yemwe Inu mudakhoza kuyankhula naye kuti atiuze ife. Chonde tilangizeni.

Pakhala pali Chakudya chochuluka chimene chayikidwa muno tsopano. Tiyeni tichigwiritse ntchito Icho. Tiyeni tichigwiritse ntchito Icho tsopano.

Kodi munthu angakhale wakhungu bwanji? Iye Amatiuza choti tichite: pa matepi pali chakudya chambiri chosungidwa; chigwiritseni ntchito TSOPANO. Ili ndi langizo la Mulungu kwa Mkwatibwi Wake.

Ngati inu mukuti inu mumakhulupirira Uthenga uwu, khulupirirani William Marrion Branham ndi mneneri wamthenga wa Mulungu wotumidwa kudzayitana Mkwatibwi; moyo wake umakwaniritsa malembo Onse omwe ananena za iye; khulupirirani ilo kuti ndi Liwu la Mulungu la tsiku lino, Kotero IYE; Mulungu, akuyankhula kupyolera mwa mneneri Wake, amamuuza Mkwatibwi mu Chichewa chomveka bwino choti achite.

Ngakhale kuti ife timasekedwa, kuzunzidwa, ndi kunyozedwa chifukwa choti ife timangomvetsera ku matepi, ife tikuchita ndendende zomwe Iye anatiuza ife kuti tichite. Zikomo Ambuye chifukwa cha Vumbulutso.

Ndikufuna kuitana dziko kuti mulumikizane nafe Lamlungu lino nthawi ya 12:00 p.m., nthawi ya ku Jeffersonville, monga tikumva: 62-1230e, “Kodi Ichi Ndi Chizindikiro Cha Mapeto, Bwana?” Tidzakhala tikumva zonse za izo :

Mabingu, Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri, Thanthwe la Piramidi, Chakudya Chauzimu, Muyaya, Kuwundana kwa Angelo, Likulu Langa, Masomphenya, Maloto, Uneneri, Zinsinsi Zobisika, Lemba pambuyo pa Lemba.

Palibe chinthu china chachikulu m’moyo uno kuposa kumva ndi kumvera Liwu la Mulungu.

M’bale. Joseph Branham

Malemba:
Malaki Chaputala 4
— Mateyu 13:3-50
Aroma 9:33; 11:25; 16:25
1 Akorinto 14:8/15 Mutu
Agalatiya 2:20
Aefeso 3:1-11 / 6:19/ 5:28-32
Akolose 4:3
1 Atesalonika 4:14-17
1 Timoteo 3:16
Ahebri 13:8
2 Petulo 2:6
Chivumbulutso 1:20 / 3:14 / 5:1 / 6:1 / 10:1-7 / 17th Chapter