25-0209 Cholinga Chofutukuka Pasanu Ndi Kamodzi Cha Gabrieli Kudzacheza Kwa Daniele

Uthenga: 61-0730E Cholinga Chofutukuka Pasanu Ndi Kamodzi Cha Gabrieli Kudzacheza Kwa Daniele

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Mkwatibwi Wa kukondwera,

Tayang’ana nkhope zathu Kumwamba m’mapemphero ndi mapembedzero kuti tipeze tsiku ndi ola lomwe tikukhalamo.

Monga sizinachitikepo kale lonse, ife tikukhala pamodzi mu malo amwambamwamba, kuchokera kuzungulira dziko, kumva Mulungu akulankhula ndi kuwulula Mawu Ake kwa ife kupyolera mwa mngelo Wake wamphamvu wamthenga. Mngelo wapadziko lapansi wamthenga yemwe Atate anamutumiza kwa Mkwatibwi Wake mu tsiku lotsiriza ili kuti awulule Mawu Ake.

Gabrieli ndi mngelo wa anthu osankhidwa a Mulungu, Ayuda. Koma kwa Mkwatibwi Wake wa Amitundu, Melkizedeki Iyemwini anabwera ndipo anayankhula kupyolera mu thupi la munthu mwa mngelo wapadziko lapansi wotchedwa William Marrion Branham, kotero kuti Iye akhoze kulankhula ndi kuwulula Mawu Ake ONSE kwa Mkwatibwi Wake wokondedwa wapamtima.

Iye anali nalo ilo likujambulidwa, kusungidwa, ndi kusamaliridwa, kotero kuti Mkwatibwi akakhale ndi Chakudya Chake chauzimu, Manna obisika, mmanja mwawo miniti iliyonse ya tsiku lirilonse mpaka mapeto a nthawi.

Mkati mwathu ndimodzazidwa ndi kudzoza komweko pomwe tikunva Liwu la Mulungu kuwulula Mawu Ake kwa ife. Momwe Iye amavumbulutsira Mawu Ake kuti tithe kuwona bwino bwino ndi kumvetsetsa tanthauzo lake. Ilo likuwulula ola lomwe tikukhalamo, Limatiuza ife amene tiri ndi chimene chiti chichitike posachedwapa; Mkwatulo wathu ukubwera posachedwa.

Iye akuwululira kwa Mkwatibwi Wake zomwe ziti zichitike pano pa dziko lapansi pamene ife tiri naye Iye pa Mgonero wa Chikwati. Momwe Iye adzatsegula maso akhungu a osankhika ake; iwo amene Iye anawachititsa khungu chifukwa cha Mkwatibwi Wake wa Amitundu.

Abwenzi anga, ndikudziwa mmene tatopela ndi dziko lino ndipo tikulakalaka za kudza kwake kudzatichotsa, koma tiyeni tisangalale ndi kuyamikira zimene zikuchitika pakali pano pamaso pathu.

Tiyeni tikweze manja athu mmwamba, mitima yathu, mawu athu, ndi kukondwera. Osati kokha kuti tikuyembekezera zimene Iye ati atichitire posachedwapa, koma tiyeni tikondwere ndi zimene Iye akutiululira ndi kutichitira ife TSOPANO.

Iye akutiuza ife kuti ndife Mkwatibwi Wake wokonzedweratu akulumikizana limodzi ndi Iye ndi Mawu Ake. Iye akutitsimikizira mobwereza bwereza, ife tiri mu Chifuniro Chake changwiro pokhala ndi Liwu Lake, Mawu Ake, mngelo Wake. Iye Watipatsa ife CHIKHULUPIRIRO chodziwa ndi kuzindikira cha chomwe Ife tiri:
MAWU AKE OKHALA MTHUPI.

Tilibe kanthu koti tizikawopa; tilibe kanthu koti tizidandaula nako; tilibe kanthu koti kazitikwiyitsa. Kodi ndikudziwa bwanji zimenezo? MULUNGU ANANENA CHOMWECHO! CHONCHO TIYENI TIKONDWERE, KHALANI OSANGALALA, KHALANI OYAMIKILA; MAWU AMOYO AMAKHAKHALA NDI KUKHALA PAKATI PATHU. NDIFE MBEWU YAKE YAPAMWAMBA YAUFUMU.

Ine Zoonadi Ndikukhulupirira kuti Ambuye akuyeneranso kukhala wokondwa kudziwa kuti nthawi yafika ndipo tadzikonzekeretsa tokha pokhala wowona ndi mokhulupirika ku Mawu Ake.

Monga mnyamata wamng’ono yemwe anayang’ana pa kalilole kwa nthawi yake yoyamba, ife tikuyang’ana mu Mawu Ake, kuwona yemwe ife TILI. Ambuye…NDI INE. Ine ndine Mkwatibwi wa Mawu Anu amoyo. Ine Ndine amene munasankha. Ine ndiri mwa Inu, Inu muli mwa ine, ndife amodzi.

Kodi Ife sutingakondwerere bwanji ndi kukhala anthu osangalala kwambiri amene anakhalapo padziko lapansi? Oyera ndi aneneri onse tisanakhalepo ife ankafuna kukhala mu tsiku lino ndi kuwona malonjezo awa akukwanilitsidwa. Koma mwa CHISOMO cha Mulungu, Iye anatiika IFE kuno.

Sitingadikire:

Uuu, mai! [M’bale Branham akuwombetsa manja ake—Mkonzi.] Psyuu! Mwa kuyankhula kwina, pamene mdani akhala atachotsedwa, mapeto a tchimo abwera, kubweretsamo kwa chilungamo chosatha kutabwera, Satana akusindikizidwira mu dzenje lopandamalire, ndipo chidziwitso cha Ambuye chidzaphimba dziko lapansi monga madzi aphimbira nyanja. Ameni! Ulemerero kwa Mulungu! Izo zikubwera, m’bale, izo zikubwera!

Kodi ndi Kudzoza kotani kumene kudzakhala kukuchitika Lamlungu pa 12:00 P.M., nthawi yaku Jeffersonville, pamene ife tidzasonkhana palimodzi kuchokera kuzungulira dziko kuti tidzamve mngelo wa Mulungu, Liwu la Mulungu kwa Mkwatibwi, kutibweretsera ife Uthenga: Cholinga Chofutukuka Pasanu ndi Kamodzi Cha Gabrieli Kudzacheza Kwa Daniele 61-0730E.

M’bale. Joseph Branham