Uthenga: 60-1225 Mphatso Yokulungidwa ya Mulungu
Wokondedwa Mkazi Wa JEZU,
O Mwanawankhosa wa Mulungu, Inu ndinu Mphatso yayikulu yokulungidwa ya Mulungu ku dziko. Inu mwatipatsa ife Mphatso yaikulu kwambiri imene inayamba yaperekedwapo, Inu eni. Inu musanalenge nyenyezi yoyamba, Inu musanalenge dziko lapansi, mwezi, mphavu ya dzuwa, Inu munatidziwa ife ndi kutisankha ife kukhala mkwatibwi wanu
Pamene Inu munatiwona ife pamenepo, Inu munatikonda ife. Ife tinali mnofu wa mnofu Wanu, fupa la fupa Lanu; ife tinali gawo la Inu. Momwe Inu munatikondera ife ndi kufuna kuyanjana nafe. Munafuna kugawana nafe Moyo Wanu Wamuyaya. Kenako Tidadziwa pamenepo, tidzakhala Anu m’kazi wa JEZU.
Inu munawona kuti ife tidzalephera, kotero Inu munayenera kutipatsa njira yotibwezeretsa ife . Tinali otayika komanso opanda chiyembekezo. Panali njira imodzi yokha, Munayenera kukhala “Chilengedwe Chatsopano”. Mulungu ndi munthu anayenera kukhala Mmodzi. Inu munayenera kuti mukhale ife, kuti ife tikhoze kukhala Inu. Chotero, Inu munaika dongosolo lanu lalikulu zaka zikwi zapitazo m’munda wa Edeni.
Inu mwakhala olakalaka kwambiri kukhala nafe, Mkwatibwi Wanu wangwiro wa Mawu, koma Inu munadziwa poyamba kuti Inu munayenera kutibwezeretsa ife ku zonse zomwe zinatayika pachiyambi. Munadikirira ndikudikirira ndi kudikirira mpaka kufikila tsiku lino kuti mumalize dongosolo Lanu.
Tsiku lafika. Kagulu kakang’ono kamene mudakawona pachiyambi kali pano. Wokondedwa wanu yemwe amakukondani Inu ndi Mawu Anu kuposa china chilichonse.
Inali nthawi yoti Inu mubwere ndi kudziulula Nokha mu thupi la umunthu monga Inu munachitira ndi Abrahamu, ndipo monga Inu munachitira pamene Inu munakhala Chirengedwe chatsopano. Momwe Inu munali kufunitsitsa za tsiku lino kotero kuti Inu mukhoze kuwulula kwa ife zinsinsi Zanu zonse zazikulu zimene zinali zobisika kuchokera ku maziko a dziko.
Inu mumanyadira kwambiri Mkwatibwi Wanu. Momwe Inu mumakondera kumuwonetsera Iye ndi kumuuza Satana, “Ziribe kanthu zomwe iwe ungayese kuchita kwa iwo, iwo sadzasuntha; iwo sadzanyengerera pa Mawu Anga, Liwu Langa. Iwo ali MKWATIBWI WANGA WA MAWU Angwiro.” Iwo ndi okongola kwambiri kwa Ine. Tangoyang’anani pa iwo! Kupyolera mu mayeso awo onse ndi mayesero, iwo amakhala okhulupirika ku Mawu Anga. ndidzawapatsa mphatso yosatha. Zonse zomwe ndili, ndipereka kwa iwo. TIDZAKHALA AMODZI.
Zonse Zomwe tinganene n’zakuti: “JEZU, TIMAKUKONDANI. Tiloleni ife tikulandireni Inu munyumba mwathu. Tiloleni ife tikudzozeni Inu ndi kusambitsani mapazi anu ndi misozi yathu ndi kuwapsyopsyona iwo. Tifuna Tikuuzeni momwe timakukonderani Inu.”
Zonse zomwe ife tili, tikupereka kwa Inu JEZU. Imeneyo ndiyo mphatso yathu kwa Inu JEZU. Timakukondani. Timakukondani Inu. Ife tikukupembedzani Inu.
Ine ndikukuitanani aliyense wa inu kuti adzakhale nafe Lamlungu pa 12:00 P.M., nthawi yaku Jeffersonville, ndi kumulandira JEZU munyumba mwanu, mu mpingo wanu, mu galimoto yanu, kulikonse kumene inu mungakhale, ndi kulandira Mphatso yaikulu kwambiri imene inayamba yapatsidwapo kwa munthu; Mulungu Mwiniwake akuyankhula ndi kuyanjana ndi inu.
M’bale. Joseph Branham
60-1225 Mphatso Yokulungidwa ya Mulungu