Uthenga: 60-1209 M’badwo Wa Mpingo Wa Sarde
- 24-1117 M’badwo Wa Mpingo Wa Sarde
- 23-0528 M’badwo Wa Mpingo Wa Sarde
- 20-1206 M’badwo Wa Mpingo Wa Sarde
- 19-0217 M’badwo Wa Mpingo Wa Sarde
- 16-0401 M’badwo Wa Mpingo Wa Sarde
Wokondedwa Anthu A Tepi,
Ndife onyadira bwanji kutchedwa “Anthu a Tepi”. Mitima yathu imathamanga ndi chisangalalo mlungu uliwonse podziwa kuti tidzakhala osonkhana Pamodzi padziko lonse lapansi pomva Liwu la Mulungu likuyankhula kwa ife.
Tikudziwa, popanda mthunzi wa chikaiko chimodzi, tili mu Chifuniro changwiro cha Mulungu pakukhala ndi Mawu Ake; kumvetsera ku Liwu Lake mwa njira ya mngelo Wake wamphamvu wamthenga wachisanu ndi chiwiri.
Mtumiki yemwe Iye anamusankha wa tsiku lathu ndi William Marrion Branham. Iye ndiye nyali ya Mulungu pa dziko lapansi, ikuunikira kuunika kwa Mulungu. Iye akuyitana mkwatibwi wosankhidwa Wake wa Mawu Oyera mwa mngelo Wake.
Mwa kuphunzira mosamalitsa kwa Mawu Ake, Iye waululira kwa ife mwa Mzimu Wake Woyera kuti William Marrion Branham ndi mngelo yemwe Iye anamusankha kuti apereke Chivumbulutso Chake ndi Utumiki kwa tsiku lathu. Ife tikuona mngelo Wake, NYENYEZI YATHU, mu dzanja Lake lamanja pamene Iye akumupatsa iye mphamvu Yake kuti awulule Mawu Ake ndi kuitana kunja Mkwatibwi Wake.
Iye watipatsa ife Vumbulutso lathunthu la Iyemwini. Mzimu Woyera kudzizindikiritsa Yekha kwa ife kupyolera mu moyo wa mtumiki Wake wa mngelo wachisanu ndi chiwiri; mngelo amene anamusankha kukhala maso ake a m’tsiku lathu lino.
Momwe mitima yathu imatenthera mkati mwathu pamene Iye amatiuza ife ndi Uthenga uliwonse kuti ndi cholinga Chake kutibweretsera ife kwa Iye mwini; kuti ndife Mkwatibwi wa Mawu Ake.
Iye amakonda kutiuza mobwereza bwereza momwe Iye anatisankhira ife asanaikidwe maziko a dziko MWA IYE. Momwe ife tinadziwidwiratu ndi kukondedwa ndi Iye.
Momwe ife timakondera kumumva Iye akuyankhula ndi kutiuza ife kuti tinawomboledwa ndi Magazi Ake ndipo MKOSATHEKA kubwera mu kutsutsidwa. Sitingakhale konse mu mchiweruzo, chifukwa tchimo silingawerengedwe kwa ife.
Momwe ife titi tidzakhale ndi Iye pamene Iye akutenga mpando Wake wachifumu wapadziko lapansi wa Davide, ndipo ife tikulamulira ndi Iye; monga anachitira kumwamba, ndi mphamvu ndi ulamuliro pa dziko lonse lapansi. Mayeso ndi mayesero a moyo uno adzawoneka ngati opanda pake.
Koma watichenjezanso za mmene tiyenera kusamala. Kuti mu mibadwo yonse mipesa iwiriyo inamera mbali ndi mbali. Momwe mdani nthawi zonse wakhala ali pafupi kwambiri; wonyenga kwambiri. Ngakhale Yudasi anasankhidwa ndi Mulungu, ndipo anaphunzitsidwa mu choonadi. Anagawana chidziwitso cha zinsinsi. Iye anali ndi utumiki wa mphamvu wopatsidwa kwa iye ndipo iye anachiritsa odwala ndi kutulutsa ziwanda mu Dzina la Yesu. Koma iye sakanakhoza kupita njira yonse.
Inu simungakhoze kupita limodzi ndi gawo chabe la Mawu, inu muyenera kutenga Mawu ONSE. Pali anthu amene amaoneka okhudzidwa ndi zinthu za Mulungu pafupifupi zana limodzi pa zana, koma satero.
Iye anati sikunali kokwanira kuti Iye wadziphatikiza Yekha ndi mpingo wonse, kapena ngakhale ndi utumiki usanu wa Aefeso 4. Iye anatichenjeza ife kuti mu m’badwo uliwonse mpingo umasokera, ndipo si anthu wamba okha komaso gulu la atsogoleri achipembedzo — abusa ali olakwa monganso nkhosa.
Chotero mwa uphungu wotsimikizirika wa chifuniro Chake chomwe, Iye anadzibweretsa Yekha powonekera mu m’badwo wathu monga M’busa Wamkulu mu utumiki wa mthenga Wake wa mngelo wachisanu ndi chiwiri kutsogolera anthu Ake kubwerera ku choonadi ndi mphamvu yochuluka ya choonadi chimenecho.
Iye ali mwa Mthenga Wake ndipo amene angakhale ndi chidzalo cha Mulungu adzatsatira Mtumiki monga Mtumikiyo ali wotsatira wa Ambuye mwa Mawu Ake.
Ine ndikufuna kukhala nacho chidzalo cha Mulungu ndi kutsatira mtumiki Wake. Kotero, kwa ife, aku m’pingo wa Branham , njira yokhayo yotsatirira mtumiki pamene iye akutsatira Ambuye mwa Mawu Ake, ndi KUSINDIKIZA KUSEWERA ndi kumva Liwu Loyera la Mulungu likulankhula kwa ife mawu osalephera.
Sitiyenera kuganiza kapena kuyang’ana zomwe tikumva, timangoyenera Kusindikiza kusewera ndikukhulupirira Mawu aliwonse omwe tikumva.
Ine ndinamumva M’bale Branham akunena mawu otsatirawa molawirira mmawa wina pa wailesi ya liwu. Nditamva Izi, zidabwera mu mtima mwanga kuti umu ndi momwe timamvera tikamati:
TIMANGOSINDIKIZA KUSEWERA NDI KUMVETSEMVERA MA TEPI.
Zinamveka ngati mawu a Chikhulupiriro chathu kwa ine.
Ndicho chifukwa ine ndimakhulupirira mu Uthenga uwu, ndi chifukwa Iwo umachokera ku Mawu a Mulungu. Ndipo chirichonse chakunja kwa Mawu a Mulungu, ine sindimakhulupirira izo. Izo zikhoza kukhala chomwecho, komabe ine ndingokhala ndi zomwe Mulungu ananena, ndiyeno ndidzakhala wotsimikiza kuti ine ndikulondola. Tsopano, Mulungu akhoza kuchita chimene Iye akufuna. Iye ndi Mulungu. Koma bola ngati ine ndikhala ndi Mawu Ake, ndiye ine ndimadziwa kuti izo nzabwino. Ndikukhulupirira zimenezo.
Ulemerero, iye anati izo ndi ZANGWIRO KWAMBIRI. Utumiki wina uliwonse ukhoza kukhala, chifukwa Mulungu akhoza kuchita zomwe Iye akufuna, ndi yemwe Iye akufuna kutero, Iye ndi Mulungu. Koma bola ngati ine ndikhala ndi Mawu Ake, Liwu Lake, Matepi, ndiye ine ndimadziwa kuti izo ndizolondola. Ndikukhulupirira zimenezo.
Ndikudziwa kuti ambiri amawerenga makalata anga ndipo samamvetsetsa zomwe ndikunena komanso zomwe ndimakhulupirira kuti ndi Chifuniro cha Ambuye kwa mpingo wathu. Ndiloleni ndinenenso modzichepetsa monga momwe mneneri ananenera kuti: “Makalata amenewa analembedwera mpingo wanga wokha. Iwo amene akukhumba kuti azitchula kuti Branham Tabernacle ndi mpingo wawo. Omwe AMAFUNA KUDZIWIKA NDI KUTCHEDWA ANTHU A TEPI”.
Ngati simukugwirizana ndi zomwe ndikunena komanso kukhulupirira, zili bwino abale ndi alongo anga. Makalata anga sanalembedwe kwa inu kapena motsutsana ndi inu kapena mipingo yanu. Mpingo wanu ndi woyima pawokha ndipo muyenera kuchita monga momwe mukumverera kuti mukutsogozedwa kuti muchite, koma molingana ndi Mawu, momwemonso kotero Uli wathu, ndipo izi ndi zomwe tikukhulupirira kuti ndi njira yoperekedwa ndi Mulungu kwa ife.
Nonse ndi olandiridwa nthawi zonse kusonkhana nafe Lamlungu lililonse pa 12:00 P.M., nthawi ya Jeffersonville. Sabata ino, Nyenyezi ya Mulungu ya m’badwo wathu, William Marrion Branham, adzakhala kutibweretsera ife Uthenga, 60-1209 M’badwo wa Mpingo wa Sardean.
M’bale. Joseph Branham