Uthenga: 63-1229E Yang’anani Kutali Kwa Yesu
- 25-1026 Yang’anani Kutali Kwa Yesu
- 24-0211 Yang’anani Kutali Kwa Yesu
- 22-0724 Yang’anani Kutali Kwa Yesu
- 20-0531 Yang’anani Kutali Kwa Yesu
- 18-0325 Yang’anani Kutali Kwa Yesu
Okondedwa Iwo Omvera Matepi,
Nthawi yafika yoti aliyense adzifunse kuti: “Ndikamamvetsera matepi, ndi Liwu lotani limene ndimamva? Kodi basi ndi Liwu la William Marrion Branham, kapena ndimamva Liwu la Mulungu la tsiku lathu? Kodi ndi liwu la munthu, kapena ndikumva Pakuti Atero Ambuye ? Kodi ndikufunika wina womasulira zomwe ndikumva, kapena kodi Mawu a Mulungu safunikira kutanthauzira?”
Yankho lathu ndi ili: Ife tikumva Mawu Olankhulidwa osandulika thupi. Tikumva Alefa ndi Omega. Tikumva Iye, Lawi la Moto, akulankhula kudzera m’milomo ya munthu monga momwe Iye ananenera kuti adzachitira m’masiku athu.
Sitimva munthu, timamva Mulungu, yemweyo dzulo, lero, ndi kwa nthawi zonse. Mawu a Mulungu omwe ndi achangu, amphamvu kuposa lupanga lakuthwa konsekonse, odula ngakhale fupa, ndi ozindikira malingaliro omwe ali mumtima.
Izo zavumbulutsidwa kwa ife kuti chimene Iye anali pamene ankayenda mu Galileya ndi chomwechi chimene Iye ali usikuuno ku Jeffersonville; chinthu chomwecho chimene Iye ali ku Branham Tabernacle. Ndi Mawu a Mulungu akuonekera. Chimene Iye anali panthawiyo, Iye ali usikuuno, ndipo adzakhalapo kwa nthawi zonse. Chimene Iye anati adzachita, Iye wachita.
Munthuyo si Mulungu, koma Mulungu akadali ndi moyo ndipo akulankhula ndi Mkwatibwi Wake kudzera mwa munthuyo. Sitiyenera kulambira munthuyo, koma kulambira Mulungu mwa munthuyo; pakuti iye ndi munthu amene Mulungu anasankha Iye kukhala LIWU LAKE ndikutsogolera Mkwatibwi Wake m’masiku otsiriza ano.
Chifukwa Iye watipatsa bvumbulutso lalikulu la nthawi yotsiriza, tsopano tikhoza kuzindikira YEMWE IFE TILI, Mawu osandulika kukhala thupi m’masiku athu ano. Satana sangatinyengenso, chifukwa ife tikudziwa kuti ndife namwali wake obwezeretsedwa mwathunthu, Mkwatibwi wa Mawu.
Liwu limenelo linatiuza kuti: Zonse zomwe ife tinkazisowa zapatsidwa kale kwa ife. Palibe chifukwa chodikira. Ilo lalankhulidwa, NDI LATHU, NDI LA IFE. Satana alibe mphamvu pa ife; wagonjetsedwa.
Inde, Satana akhoza kutibweretsera matenda, kuvutika maganizo, ndi chisoni, koma Atate watipatsa kale mphamvu yoti timutulutsire kunja…IFE TIMANGOLANKHULA KOKHA MAWU, Ndipo iye ayenera kutichokera….osati chifukwa chakuti ife tanena choncho, koma chifukwa chakuti MULUNGU ANANENA CHONCHO.
Mulungu yemweyo amene analenga agologolo, pamene panalibe agologolo. Zimenezo zinamupatsa Mlongo Hattie chofuna cha mtima wake: ana ake aamuna awiri. Amene anachiritsa Mlongo Branham chotupa dzanja la dokotala lisanamukhudze. Iye ndi MULUNGU YEMWEYO amene sali ndi ife kokha, KOMASO IYE ALI NDI MOYO NDIPO AKUKHALA MWA IFE. IFE NDIFE MAWU OSANDULIKA KUKHALA THUPI.
Tikamaona ndi kumvetsera Mawu pa matepi, timaona ndi kumva Mulungu akudziulula Yekha mu thupi la munthu. Timaona ndi kumva amene Mulungu anatuma kuti atitsogolere ku Dziko Lolonjezedwa. Timadziwa kuti Mkwatibwi yekha ndiye adzakhala ndi bvumbulutso limenero, motero takhala opanda mantha. Palibe chifukwa chokhala ndi manjenje, kuvutika maganizo, kukhumudwa, kudabwa kapena kuda nkhawa…NDIFE MKWATIBWI.
Mvetserani ndi kukhala ndi moyo, m’bale wanga, khalani ndi moyo!
Mvetserani Yesu tsopano ndi kukhala ndi moyo;
Pakuti zajambulidwa pa matepi, aleluya!
Ndi kuti timvetsere ndikukhala ndi moyo.
O, Mkwatibwi wa Yesu Khristu, ndi tsiku lalikulu bwanji lomwe tikukhalamo. Zimene tikuyembekezera, mphindi ndi mphindi. Tsiku lililonse tsopano tidzawona okondedwa athu, ndiye, mu mphindi ya kuthwanima kwa diso, tidzachoka pano ndipo tidzakhala nawo mbali ina. Zili moyandikira kwambiri kotero kuti zikuwoneka kuti tingazikhudze izo…ULEMERERO!
Bwerani Mkwatibwi, tiyeni tisonkhanenso mozungulira Mawu a Mulungu Lamlungu lino nthawi ya 12:00 PM, nthawi ya ku Jeffersonville, pamene Ife tikumumva Iye akulankhula nafe Mawu a Moyo Wamuyaya.
M’bale. Joseph Branham
Uthenga: 63-1229E Yang’anani Kutali Kwa Yesu
Malemba Opatulika:
Numeri 21:5-19
Yesaya 45:22
Zekariya 12:10
Yohane Woyera 14:12