25-1012 Kusimidwa

Uthenga: 63-0901E Kusimidwa

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Mkwatibwi wa Tepi,

Tsopano inu anthu mu matepi kumeneko.

Ambuye, ife tingayambe bwanji kufotokoza chimene mawu aang’ono asanu ndi limodzi awa akutanthauza kwa ife, Mkwatibwi wa Yesu Khristu? Ndi Vumbulutso la Uthenga wa orali kwa ife. Ndi Mulungu akuyankhula kupyolera mwa m’thenga Wake wa mngelo kumuuza Mkwatibwi Wake, “Ine ndikudziwa inu mudzakhala ndi Liwu Langa. Ine ndikudziwa chimene Mawu Anga pa matepi awa ati adzatanthauze kwa inu.Ine ndikudziwa inu mudzakhala ndi Vumbulutso kuti Mauthenga awa amene ine ndawayankhula mu matepi ali Chizindikiro Changa cha lero.”

“Ine ndaika Liwu Langa pa matepi a maginito awa; pakuti Mauthenga awa ayenera kutsirizitsa Mawu onse. Padzakhala zikwi kuchulukitsa zikwi amene ati adzamve Liwu Langa pa matepi ndipo adzakhala ndi Vumbulutso kuti uwu ndi utumiki Wanga.Ndi mzimu woyera wa lero. Ndi uthenga wanga wa chizindikiro

“Ine ndatumiza atumiki okhulupirika ambiri ku dziko lonse lapansi kuti akalengeze utumiki Wanga. Pamene iwo anabwerera, iwo anandiuza Ine, ‘Ife tamvera malamulo Anu mwa kusewera matepi Anu.Ife tinapeza anthu amene amakhulupirira Mawu aliwonse. Iwo apanga nyumba za Iwo eni kukhala tchalitchi zolandiliramo Uthenga Wanu. Ife tinawauza iwo, onse amene akanadzabwera pansi pa Chizindikiro Chanu, Uthenga wa orali, akanadzapulumutsidwa.’”

Ndi nthawi yomwe munthu aliyense ayenera kudzifufuza ndikudzifunsa yekha, kodi njira yangwiro ya Mulungu lero ino ndi iti? Mawu a mneneri sanalepherepo nthawi imodzi. Icho chatsimikiziridwa kuti ndi Choonadi CHOKHA, CHINTHU CHOKHAKO chimene chiti chidzamuyanjanitse Mkwatibwi Wake.

Chirichonse chimene iye ananena chachitika ndendende basi momwe iye ananenera icho. Lawi la Moto likadali pano ndi ife.Liwu la Mulungu akuyankhulabe ndi ife pa matepi. Mneneri anangotiuza ife kuti Mulungu analambala pamwamba kokha pamene Iye adawona Chizindikiro. Ndi nthawi ya kusimidwa kuti onse alowe pansi pa Uthenga wa Chizindikiro uwo.

Ife taliwona Dzanja lamphavu la Mulungu mu nthawi yotsiriza ino. Iye watipatsa ife Vumbulutso loona la Mawu Ake ndipo ilo labwera pansi pa chisonyezo cha Chizindikiro. Tsopano, pamene ife tiri pansi pa chisonyezo cha Chizindikiro, tiyeni ife tibwere palimodzi ndi kudya Mgonero mwa kusimidwa; pakuti tidziwa kuti Mulungu akukozekera kuti akanthe ndi chiweruzo.

Ndikufuna kuitana aliyense wa inu kuti mumve ndi kukhala ndi M’gonero ndi Utumiki wosambitsana Mapazi Lamlungu lino, pamene tikumva Uthenga: Kusimidwa 63-0901E.

Uthenga ndi utumiki wa Mgonero udzakhala pa Wailesi Ya Liwu kuyambira 5:00 P.M. nthawi ya ku Jeffersonville . Chonde khalani omasuka kukhala ndi chiyanjano chanu nthawi ya kwanuko ngati mungafune, monga ndikudziwira kuti zidzapangitsa kukhala kovuta kwa okhulupirira athu ambiri akunja kuyamba chiyanjano chawo panthawiyo. Padzakhala ulalo wa fayilo yotsitsika ya utumiki.

M’bale. Joseph Branham

Malemba oti muwerenge musanayambe chiyanjano:

Ekisodo 12:11
Yeremiya 29:10-14
Luka 16:16 St
Yohane 14:23
Agalatiya 5:6
Yakobo 5:16