25-1005 Chizindikiro

Uthenga: 63-0901M Chizindikiro

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Mkwatibwi Wa Chizindikiro

Pamene ife tibwera palimodzi, ife sitimangoyankhula za Uthenga, ife timabwera palimodzi kuti tidzaike Magazi, kuti tiike Chizindikiro; ndipo Chizindikiro ndi Uthenga wa orali! Ndiwo Uthenga wa tsiku lino! Ndiwo Uthenga wa nthawi ino.

Ife tayika Chizindikiro icho kwa ife eni, ku nyumba zathu, ndi kwa mabanja athu. Sitikuchita manyazi. Sitisamala amene akudziwa. Tikufuna kuti aliyense adziwe, wodutsa aliyense awone ndi kudziwa: Ndife Anthu a atepi. Ndife a Tepi yapa nyumba . Ndife Mkwatibwi wa Tepi wa Mulungu.

Mzimu Woyera = Chizindikiro = Uthenga. Onse ali ofanana. Simungathe kuwalekanitsa. Atate, Mwana, Mzimu Woyera = Ambuye Yesu Khristu. Simungathe kuwalekanitsa. Uthenga = Mtumiki. Ziribe kanthu zomwe otsutsa anena, M’NENERI ANATI, inu simungakhoze kuwalekanitsa iwo.

Mulungu ndiye chimwemwe chanu. Mulungu ndiye mphamvu yanu. Kudziwa Uthenga uwu, kudziwa kuti Iwo ndi Choonadi chokha, kudziwa kuti Icho ndi Chizindikiro, ndiko kukwanira kwathu. Ena akhoza kunena, “Ine ndimawakhulupirira Iwo, ine ndimawakhulupirira Iwo, ine ndikukhulupirira Iwo ndi Choonadi. Izo zonse nzabwino, komabe Izo ziyenera kuyikidwa.

Mneneri anati Uthenga uwu ndi Chizindikiro cha lero. Uthenga uwu ndi Mzimu Woyera. Ngati inu muli ndi Vumbulutso lirilonse la Uthenga uwu inu mukhoza kuwona momveka ora limene ife tikukhalamoli. Ochuluka kwambiri akunena, “Ine ndikukhulupirira Iwo. Mulungu anatumiza mneneri. Iwo uli Uthenga wa ora,” koma Iwo amadzitama ponena kuti iwo satero, ndipo sadzatero, kusewera Liwu lomwe la Chizindikiro mu mipingo yawo.

Mulungu sanalankhule kupyolera mwa mngelo Wake wamphamvu ndi kungonena chinachake pokhapokha ngati chinali ndi tanthauzo. Iye anatiuza ife kuti anatiphunzitsa ife mwa zoimira ndi mithunzi. Mu Uthenga uwu, mneneriyu akufotokoza mwatsatanetsatane kutiuza zimene Rahabi ndi a banja lake anachita kuti apulumutsidwe, kuti akhale Mkwatibwi. Anafotoza momveka bwino pa zomwe mkaziyo anachita.

Pamene anyamata a tepi ankasewera “TEPI”…Dikirani miniti, kodi mthenga uja anachita chiyani? Anasewera Tepi. Ndiye kodi iye anachita chiyani? Anayipanga iye nyumba yake MPINGO WA TEPI. Iye sanachite manyazi kunena kuti, “Onani chingwe chofiyira icho, izo zikutanthauza kuti ine ndine wa MPINGO WA TEPI”.

Inu mukuganiza ngati iye akanati, “Inde, ine ndikumukhulupirira m’thenga ndi Uthenga, koma ife sitimaseweranso Matepi ndipang’ono pomwe mu mpingo wathu. Ndili ndi m’busa amene amati AYI, iyeyo ayenera kungolalikira ndi kubwereza zomwe matepi amanena.” Inu mukuganiza kuti mkazi uja akanapulumutsidwa…???

Iye anaika chizindikiro, ndipo nyumba yake inapulumutsidwa, kapena iye akanawonongeka kumusi uko komwe iye anali.

Mwamvapo atumiki ambiri akupereka zifukwa zodzikhululukira ponena za kusewera matepiwo, koma ambiri a iwo amati: “Mneneri sananenepo kuti azisewera matepiwo m’tchalitchi.”

Mneneri anati Rahabu anayipanga iye nyumba yake kukhala tchalitchi, ndipo mpingo wake unkasewera Matepiwo. Ndipo chifukwa chakuti iye ankasewera Matepi mu mpingo wake, iye, ndi Mpingo wake wonse wa TEPI, anali pansi pa Chizindikiro ndipo anapulumutsidwa. Mpingo wina uliwonse unawonongeka.

Abale ndi alongo, chonde, ine sindikunena kuti m’busa sangakhoze kulalikira Uthenga uwu, kapena kuti ndi zolakwika ngati iye atero. Mwa njira yanga yanga, Ine ndikulalikira tsopano kupyolera mu kalata iyi, koma tsegulani mtima wanu ndi kumvetsera zimene mneneri akunena ndi kukuchenjezani inu. Ngati m’busa wanu akukana, kapena adzakana, kuti azisewera matepi mu mpingo wanu pakupanga chowiringula cha mtundu wina; chirichonse chimene chingakhoze kukhala ziribe kanthu kuchuluka kwa zomwe iye anena “Ine ndikukhulupirira Uthenga wa orali,” molingana ndi zomwe ine ndikukhulupirira Mawu akunena, Chizindikiro, Uthenga wa orali, iwo sukuyikidwa.

Lamlungu lino, ine ndikukuitanani inu kuti mubwere mudzamvetsere ndi Branham Tabernacle pa 12:00 p.M., nthawi ya ku Jeffersonville, ku Uthenga: Chizindikiro 63-0901M. Ngati inu simungakhoze kutijowina ife, sewerani Uthenga wa Chizindikiro uliwonse, ndi kuwuyika Iwo.

M’bale. Joseph Branham

Malemba oti muwerenge musanamve Uthenga:

Genesis 4:10
Ekisodo chaputala 12
Yoswa mutu 12
Machitidwe 16:31/19:1-7
Aroma 8:1
1 Akorinto 12:13
Aefeso 2:12/4:30
Ahebri 6:4 / 9:11-14 / 10:26-29 / 11:37 / 12:24 / 13:8, 10-20
Yohane 14:12