25-0727 Mkwatulo

Uthenga: 65-1204 Mkwatulo

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Mkwatibwi Wopanda mangawa,
 
 
Ambuye anatipatsa ife nthawi yodabwitsa kwambiri pa msasa sabata yatha pamene Iye anatiululira Mau ake kwa ife. Iye anatsimikizira, mwa Mawu Ake, kuti Mtheradi wathu uli: Mawu Ake, Uthenga uwu, Liwu la Mulungu pa matepi; onse ali ofanana, Yesu Kristu yemweyo dzulo, lero, ndi kunthawi zonse. 
 
Tinamva mmene mdierekezi amayesera kulekanitsa Uthenga kwa mthengayo, koma Ambuye Yesu alemekezeke, Mulungu mwini analankhula kudzera mwa mngelo wake wamphamvu natiuza kuti:

Ife tikupeza apo kuti pamene munthu abwera, atatumidwa kuchokera kwa Mulungu, wodzozedwa ndi Mulungu, ndi PAKUTI ATERO AMBUYE woona, uthenga ndi mtumiki ali mmodzi ndi ofanana. Chifukwa iye watumidwa kuti adzayimire PAKUTI ATERO AMBUYE, Mawu ndi Mawu, kotero iye ndi uthenga wake ali ofanana.

Inu simungakhoze kulekanitsa Uthenga kwa mtumikiyo, iwo ali ofanana, PAKUTI ATERO AMBUYE. Ziribe kanthu zomwe wodzozedwa wabodza aliyense akunena, Mulungu anati iwo ali ofanana ndipo sangalekanitsidwe.
 
Ndiye Iye anatiuza ife kuti sitikusowa chiguduli chosefera kuti tigwire zipumbu zonse pomwe ife tikumvetsera ku matepi, pakuti mulibe nsikidzi kapena madzi a sikidzi mu Uthenga uwu. Ndi chitsime Chake cha kasupe chomwe chimayenda madzi nthawi zonse oyera ndi awukhondo. Nthawizonse akutumphukabe pamwamba, sichimawuma ayi, kumangopitirira kukankhira ndi kukankha, kumatipatsa ife Vumbulutso lochulukira la Mawu Ake.
 
Anatikumbutsa kuti tisaiwale kuti pangano lake ndi ife ndi Losatsutsika, Losatsutsika, koma koposa zonse, Lopanda mangawa.
 
Kaya ndi chikondi, chithandizo, kapena kugonja, ngati china chake chopanda mangawa ndi MTHERADI ndipo sichigwirizana ndi mfundo kapena zikhalidwe zina zapadera: izo zichitika zivute zitani.
 
 Ndiye Iye anafuna kukhomerera msomali, kotero anatiuza ife kuti lero Malemba Ake akukwaniritsidwa pamaso pathu.

Kuti d-z-u-w-a lomwelo limene limatuluka kummawa ndi d-z-u-w-a lomwelo limene limadzalowa kumadzulo. Ndipo M-w-a-n-a wa Mulungu yemweyo amene anabwera kummawa ndi kudzadzitsimikizira Yekha ngati Mulungu wowonetseredwa mu thupi, ndi M-w-a-n-a wa Mulungu yemweyo kumadzulo kwa dziko lapansi kuno, amene akudzizindikiritsa Yekha pakati pa mpingo usikuuno, yemweyo dzulo, lero, ndi kwanthawizonse. Kuwala kwa kumadzulo kwa Mwana kwafika. Lero Lemba ili lakwaniritsidwa pamaso pathu.

 Mwana wa Munthu wabweranso mu thupi laumunthu mu tsiku lathu, monga momwe Iye analonjezera kuti Iye akanadzatero, kuti adzaitane Mkwatibwi. Ndi Yesu Khristu akuyankhula molunjika kwa ife, ndipo Izo sizikusowa kutanthauzira kwa munthu. Zonse zomwe tikusowa, zomwe tikufuna, ndi Liwu la Mulungu loyankhula pa tepi lochokera kwa Mulungu Mwiniwake.

Ndi vumbulutso la kukwaniritsika kwa Mawu kukhalitsidwa owona. Ndipo ife tikukhala mu tsiku limenelo. Mulungu alemekezeke! Vumbulutso la chinsinsi la Iyemwini.

Ndi nthawi yaulemerero bwanji yomwe Mkwatibwi ali nayo, ali mu kukhalapo kwa Mwana, akucha. Tirigu wabwereranso ku tirigu, ndipo palibe chotupitsa pakati pathu. Liwu loyera la Mulungu loyankhula kwa ife, kutiumba ndi kutipanga ife mu chifaniziro cha Khristu, Mawu.
 
 
Ife ndife ana aamuna ndi aakazi a Mulungu, chikhumbo Chake chimene Iye anachikonzeratu kuti chibwere mu m’badwo uno, m’badwo waukulu kwambiri mu mbiriyakale ya dziko.  Iye ankadziwa kuti ife sitikanati tilephere, ife sitikanati tinyengerere, koma ife tikanakhala Mkwatibwi Wake wa Mawu owona ndi wokhulupirika, Mbewu Yake Yachifumu yolonjezedwa Yapamwamba ya Abrahamu yomwe inali nkudza.
 
Mkwatulo uli pafupi. Nthawi yafika kumapeto. Iye akudzera Mkwatibwi Wake yemwe wadzikonzekeretsa Yekha koma akukhala mu Kukhalapo kwa Mwana, akumva Liwu Lake kumuveka Mkwatibwi Wake. Posachedwapa tidzayamba kuona okondedwa athu omwe ali kuseri kwa ketani ya nthawi, omwe akuyembekezera ndi kulakalaka kukhala nafe.

Matepi ndi njira yoperekedwa ndi Mulungu kuti afikitse Mkwatibwi Wake ku ungwiro. Matepi awa ali chinthu chokha chimene chidzagwirizanitsa Mkwatibwi Wake. Matepi awa ali Liwu la Mulungu kwa Mkwatibwi Wake.
 
Ine ndikukuitanani inu kuti mubwere ndi kudzalumikizana nafe, gawo la Mkwatibwi Wake, Lamlungu lino pa 12:00 p.m., nthawi ya ku Jeffersonville, pamene ife tikumva zonse za zomwe zikukonzekera kuti zichitike posachedwapa: Mkwatulo 65-1204. 

 
M’bale. Joseph Branham