25-0713 Malo Okhawo Operekedwa Ndi Mulungu Opembedzerapo

Uthenga: 65-1128M Malo Okhawo Operekedwa Ndi Mulungu Opembedzerapo

PDF

BranhamTabernacle.org

Lokondedwa Banja la Yesu Khristu,

Chinachake chikuchitika kuposa kale ndi Mkwatibwi wa Khristu padziko lonse lapansi. Zinthu zomwe tazimva ndi kulakalaka kuziwona tsopano zikuwonetseredwa pamaso pathu.

Mzimu Woyera ukugwirizanitsa Mkwatibwi Wake monga Iye anati Iye akanadzatero, mwa njira Yake YOKHA yoperekedwa ya lero, Liwu la Mulungu pa matepi.

Iye akuwulula ndi kutsimikizira Mawu Ake kuposa kale. Mofanana ndi chitsime cha kasupe, Chibvumbulutso chikutumphuka mkati mwathu.

Chilumikizano chauzimu chija cha Khristu ndi Mpingo Wake tsopano, pamene mnofu ukusandulika Mawu, ndipo Mawu akusandulika mnofu, kuwonetseredwa, kutsimikiziridwa. Basi zomwe Baibulo linati zikanadzachitika mu tsiku lino, izo zikuchitika, tsiku ndi tsiku. Bwanji, izo zikuwunjikana mofulumira kwambiri kunja uko, mu zipululu izo, ndi zinthu zomwe zikuchitika, mokuti ine sindingakhoze ngakhale kuyendera limodzi nazo izo.

Tsiku ndi tsiku Chivumbulutso chochuluka chikuwululidwa ndikuwonetseredwa kwa ife. Monga mneneri, zinthu zikuchitika ndipo zikuchitika mofulumira kwambiri, sitingathe ngakhale kupitiriza nazo … ULEMERERO!!!

Nthawi yathu yafika. Lemba likukwaniritsidwa. Thupi likukhala Mawu, ndipo Mawu akukhala thupi. Basi zomwe mneneri ananena kuti zikanadzachitika tsopano zikuchitika.

Kodi ndi Chifukwa chiyani ife?

Palibe chotupitsa, kapena mawu osadziwika, palibe kutanthauzira kwa munthu kofunika pakati pathu. Timangomvetsera Mawu Oyera Angwiro kuchokera mkamwa mwa Mulungu pamene Iye akulankhula kwa ife milomo ndi khutu.

Tsopano ife tikuwaona Mawu olonjezedwa omwewo, a Luka, a Malaki, malonjezo onse awa kuyambira lero, akupangidwa thupi, akukhala pakati pa ife, amene ife tinawamva ndi makutu athu; tsopano ife tikumuwona Iye (ndi maso athu) akutanthauzira Mawu Ake Omwe, ife sitikusowa kutanthauzira kulikonse kwa munthu.

Mkwatibwi, izo mophweka sizikanakhoza kumveka bwino kuposa izo. Iye ndi Mulungu, atayima pamaso pa Mkwatibwi Wake mu thupi laumunthu, yemwe ife tikhoza kumuwona ndi maso athu omwe, akuyankhula ndi kutanthauzira Mawu Ake Omwe, ndi kuwayika iwo pa tepi. Mawu Angwiro olankhulidwa ndi kulembedwa ndi Mulungu Mwiniwake, motero samasowa kutanthauzira kulikonse kwa munthu.

  • Mulungu akuyankhula molunjika kwa Mkwatibwi Wake, pa matepi.
  • Mulungu akutanthauzira Mawu Ake Omwe, pa matepi.
  • Mulungu akudziwulula Yekha, pa matepi.
  • Mulungu akumuuza Mkwatibwi Wake, inu simukusowa kutanthauzira kulikonse kwa munthu, Mawu Anga pa matepi ali zonse ZOFUNIKIRA MKWATIBWI WANGA.

Kumbukirani, pamene inu muchoka pano, muyambe kuchokamo mu mankhusu tsopano; inu mukupita mu njere, koma mukakhale mu Kukhalapo kwa Mwana. Musakawonjezere, zimene ine ndanena; musakachotsere, zimene ine ndanena. Chifukwa, ine ndimayankhula Choonadi monga momwe ine ndikudziwira Icho, monga Atate andipatsira ine. Mukuona?

Mulungu wapanga NJIRA YABWINO YOKHAYO kuti Mkwatibwi achite monga momwe anatilamulira ife. Izi sizinachitikepo, mpaka lero. Palibe kungoganiza, popanda kudabwa, palibe funso ngati pali china chowonjezera, chochotsedwa, kapena kutanthauzira. Mkwatibwi wapatsidwa Chibvumbulutso chenicheni: KUSEWERA MATEPI NDI NJIRA YABWINO YA MULUNGU.

Ngati zingachitike, ndiroleni ndinenenso. Vumbulutso langa liri kuti Mkwatibwi wa Yesu Khristu, osati ena, MKWATIBWI, sasowa CHINTHU CHINA CHILICHONSE AYI koma Liwu la Mulungu pa matepi.

Koma pamene Mzimu Woyera uwo kwenikweni Mawu enieni abwera mwa inu (Mawu, Yesu), ndiye, m’bale, Uthenga si chinsinsi kwa inu kenako; inu mukuchidziwa Icho, m’bale, Icho chonse chawala pamaso panu.

Uthenga si chinsinsi kwa ine. Yesu Khristu ali yemweyo dzulo, lero, ndi kunthawi zonse. Kumwamba ndi dziko lonse lapansi zimatchedwa Yesu. Yesu ndiye Mawu.

Ndipo Dzinalo liri mu Mawu chifukwa Iye ali Mawu. Ameni! Iye ndi chiyani ndiye? Mawu otanthauziridwa ndi mawonetseredwe a Dzina la Mulungu.

Mulungu akulumikiza Mkwatibwi Wake ndi Liwu Lake, limene Iye analilemba ndi kulisungira kwa lero, kotero kuti Iye akhoze kubweretsa Mkwatibwi Wake palimodzi ngati Chigawo Chimodzi. Mkwatibwi aziwona izo ndi kuzizindikira Iyo ngati NJIRA YOKHAYO yomwe Iye angakhoze kubweretsa Mkwatibwi Wake palimodzi.

Iye anachita zimenezi zaka zoposa 60 zapitazo kuti atisonyeze mmene angachitire zimenezi masiku ano. Ndife “m’modzi mwa mipingo yake yomwe ikugwirizana”

Ngati ine sindikhulupirira mu kupita kutchalitchi, nchifukwa chiyani ine ndiri ndi tchalitchi? Ife tinali nawo iwo onse kudutsa m’dzikoli, titalumikizitsana usiku wina, mailosi thuu handiredi aliwonse a mabwalo anali ndi imodzi ya matchalitchi anga.

Atumiki ambiri amauza mipingo yawo kukhala pa “kulumikizana” kapena “kukhamukira”, “kumvera Uthenga womwewo nthawi imodzi”, sikupita kutchalitchi. IYE ANANGOTI IZO ZINALI! Iwo mwina sakudziwa Mawu kapena sangathe kuwerenga kalata yachikondi monga Mkwatibwi angachitire.

Kodi mpingo ndi chiyani? Tiyeni tingowona zomwe M’bale Branham ananena kuti zinali mpingo.

Magulu ambirimbiri, ali nawo malo awa omwe inu nonse munali nawo kuno kuchokera ku kachisi. Izo zalumikizidwanso ku Phoenix, kuti kulikonse kuli msonkhano, izo zikufika kumene umo…Ndipo iwo akusonkhana mu matchalitchi ndi mmanyumba, ndi zinthu monga choncho, zikudutsa mu mpweya wa mawu wabwino kwambiri.

M’bale Branham akunena momveka bwino kuti anthu mu “nyumba” zawo ndi “zinthu zonga izo” inali imodzi mwa mipingo yake yomwe inali yolumikizana. Motero nyumba, malo opangira mafuta, nyumba, mabanja osonkhanitsidwa pamodzi pa hook up ake anapanga mpingo.

Tiyeni tiwerenge KALATA YA CHIKONDI mwakanthawi kochurukilapo pang’ono

Ife tikupempherera mipingo yonse ndi magulu amene asonkhana pozungulira zo—zo—zoyankhulira zazing’ono kunja kudutsa, kuchokera ku fukoli, njira yonse mpaka ku Gombe la Kumadzulo, kukwera mpaka ku mapiri a Arizona, kutsika mpaka ku zigwa za Texas, njira yonse mpaka ku Gombe la Kummawa, monse kudutsa dziko, Ambuye, kumene iwo asonkhana. Maora ambiri motalikana, ife tiri mu nthawi, koma, Ambuye, ife tiri limodzi usikuuno ngati chimango chimodzi, okhulupirira, tikuyembekezera Kudza kwa Mesiya.

Kotero kukhala pa Kulumikizana, kumvetsera kwa M’bale Branham ONSE PA NTHAWI YOFANANA; iwo anali pamodzi ngati gulu limodzi, okhulupirira, kuyembekezera Kudza kwa Mesiya.

Koma mukunena kuti ngati muchita izi lero, kuti uko sindiko kupita kutchalitchi, izo ndizolakwika, sikumasonkhana pamodzi monga momwe tikuwonera tsiku likuyandikira, sikupita kutchalitchi kodi?

Ndiroleni ine ndikufunseni inu funso ndipo inu muwayankhe osonkhana anu. Ngati M’bale Branham akanakhala pano lero, mu thupi, ndipo inu mukanakhoza kukhamukira kapena kulumikizana kuti mumumve iye Lamlungu lirilonse mmawa, Onse pa nthawi imodzi ndi Mkwatibwi kuzungulira dziko, azibusa, kodi inu mungagwirizane ndi kumumva M’bale Branham kapena kodi inu mungalalikire?

M’bale Branham momveka akunena kuti ntchito yanu ndi mpingo wanu. Ngati inu munali kuno zaka makumi asanu ndi chimodzi zapitazo ndipo M’bale Branham anali ndi utumiki, koma mpingo wanu sunapiteko koma kukhala ndi utumiki wawo (umene atumiki ambiri ankachitira kalelo), kodi inu mungapite ku “mpingo wanu”, kapena kodi inu mungapite ku “Branham Tabernacle” kuti mukamve M’bale Branham?

Ndikupatsani yankho langa. Ine ndikanakhala nditaima pakhomo mu mvula, matalala kapena mphepo yamkuntho kuti ndilowe mu Kachisi kuti ndimve mneneri wa Mulungu. Ngati ndikanapita ku mpingo wina uja, ndikanasintha matchalitchi usiku womwewo.

Koma mkazi ameneyo, iye sankadziwa ngati mphamvu inali mu ndodo kapena ayi, koma iye ankadziwa kuti Mulungu anali mwa Eliya. Ndiko kumene Mulungu anali: mwa mneneri Wake. Iye anati, “Monga Ambuye ali wa moyo, ndiye kuti solo yanuso ili moyo, ine sindidzakusiyani inu.”

Ine ndikukuitanani inu kuti mutijowine ife ndi kukhala mmodzi wa mipingo ya M’bale Branham pa nthawi yolumikizirana Lamlungu 12:00 P.M., nthawi ya ku Jeffersonville, pamene ife tikumva Liwu la Mulungu likutibweretsera ife Uthenga: Malo Okhawo Operekedwa Ndi Mulungu Opembedzerapo 65-1128M.

M’bale. Joseph Branham