25-0706 Ine Ndakhala Ndikumva Koma Tsopano Ine Ndawona

Uthenga: 65-1127E Ine Ndakhala Ndikumva Koma Tsopano Ine Ndawona

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Mkwatibwi Wolumikizidwa,

Lero, Mawu awa amene Mulungu analankhula kupyolera mwa Mngelo Wake Wachisanu ndi chiwiri akukwaniritsidwabe kupyolera mwa IFE, MKWATIBWI WA YESU KHRISTU.

Ngati ine sindikhulupirira mu kupita kutchalitchi, nchifukwa chiyani ine ndiri ndi tchalitchi? Ife tinali nawo iwo onse kudutsa m’dzikoli, titalumikizitsana usiku wina, mailosi thuu handiredi aliwonse a mabwalo anali ndi imodzi ya matchalitchi anga.

Iwo anali m’matchalitchi, m’nyumba, m’nyumba zing’onozing’ono, ndipo ngakhale pokwerera mafuta; anamwazikana kudutsa United States, akumvetsera, zonse pa nthawi imodzi yomweyo pomwe Mawu anali kupita.

Ndipo lero, ife tikadali MMODZI WA MIPINGO YAKE. Iye akadali M’BUSA WATHU. Mawu Ake SAMASOWABE KUTANTHAUZIDWA, ndipo ife tikanali osonkhanitsidwa pa dziko lonse, WOl pa MODZI, kumvetsera ku LIWU la Mulungu kumupanga kukhala wa gwiro Mkwatibwi wa Yesu Khristu.

Lero, Mawu awa akukwaniritsidwabe.

N’cifukwa ciani anali kucita zimenezo kalelo? Chifukwa chiyani abusa anatseka mipingo yawo kuti asamvere Uthenga nthawi yomweyo? Iwo akanangoyembekezera kuti atenge matepi, ndiyeno nkumalalikira Uthenga iwoeni kwa anthu awo kenako; ndipo ndikutsimikiza kuti ambiri opanda bvumbulutso Ankachita izi.

Kapena mwinamwake ena adawuza mipingo yawo, “Tsopano mvetserani, ife timakhulupirira M’bale Branham kuti ndi mneneri wa Mulungu, koma iye sananene kuti ife timayenera kumamvetsera kwa iye mu mipingo yathu. Ine ndikulalikira Lamlungu lino, ndi Lamlungu lirilonse;

Kenako Mkwatibwi , monga Mkwatibwi chabe tsopano, anali ndi Vumbulutso, ndipo ankafuna kumva Liwu la Mulungu mwachinjunji kwa iwo eni. Iwo ankafuna kuti akhale olumikizana ndi Mkwatibwi kuzungulira dziko kuti amve Liwu la Mulungu pamene ilo linali kunveka. Iwo ankafuna kuti azindikiritsidwe ngati umodzi wa mipingo yake, nyumba, kapena kulikonse kumene iwo anali, ndi Uthenga, Liwu, ndipo tsopano matepi.

Lero, Mawu awa akukwaniritsidwabe.

Chifukwa chiyani iwo/ife tinachiwona Icho ndipo ena sanachiwone? Mwa kudziwiratu, ife tinadzozedweratu kuti tiziwone Izi. Koma inu amene simunadzozedwe, simudzaziwona konse Izo. Tirigu akuwawona Iwo ndipo wayamba kuchokapo.

Izi sizikutanthauza kuti muyenera kusiya kupita kutchalitchi chanu. Komanso sizikutanthauza kuti abusa anu asiye kutumikira. Mophweka izi Zikutanthauza kuti mautumiki ambiri ndi azibusa aiwala CHINTHU CHENICHENI, ndiko kusawawuza anthu awo kuti MAWU OFUNIKA KWAMBIRI omwe muyenera kuwamva ndi LIWU la Mulungu pa matepi.

Kupita ku tchalitchi tsiku lililonse sabata iliyonse sikukupanga iwe kukhala Mkwatibwi; chimenecho sichofunikira cha Mulungu. Afarisi ndi Asaduki anali ndi chiphunzitso chimenecho kumusi uko. Iwo ankadziwa chilembo chirichonse cha Mawu aliwonse, koma Mawu Amoyo anali ataima POMWEPO mu thupi la munthu, koma kodi iwo anachita chiyani? Chinthu chomwecho chimene ambiri amachita lerolino.

Iwo amati, “Izo zinali zipembedzo zimene iye anali kuzikamba.” Iwo samamulola M’bale Branham mu mipingo yawo kuti azilalikira, koma ife timalalikira Mawu ndi kunena mobwereza basi zomwe iye ananena.

Izi ndizodabwitsa. Ambuye alemekezeke. Ndi zomwe muyenera kuchita. Koma Kenako mkumati, lero ndi zosiyana, ndi zolakwika kumasewera matepi a M’bale Branham mu tchalitchi chanu. Inu apo simuli osiyana ndi Afarisi ndi Asaduki, kapena zipembedzo.

Ndiwe wa chinyengo.

Monga zinaliri pamenepo, Ndi Yesu, atayima pakhomo akugogoda, kuyesera kuti alowe kuti ayankhule mwachinjunji kwa Mpingo Wake, ndipo iwo sadzatsegula zitseko zawo, ndipo sadzasewera matepi mu mipingo yawo. “Iye sakubwera mu mpingo wathu ndi kudzalalikira”.

Mdaniyo azipotoza izo ndikuzivunguza mbali zochuruka momwe iye AMADANA ndikuyalutsidwa, komabe, zikuwonekera pamaso pathu pomwe ndipo ambiri akuchoka.

“Pa chiyambi panali” [Osonkhana ati, “Mawu”—Mkonzi.] “ndipo Mawu anali ndi” [“Mulungu,”] “Ndipo Mawu anali” [“Mulungu.”] “Ndipo Mawu anapangidwa thupi ndipo anadzakhala pakati pathu.” Ndi kulondola uko? Tsopano ife tikuwaona Mawu olonjezedwa omwewo, a Luka, a Malaki, malonjezo onse awa kuyambira lero, akupangidwa thupi, akukhala pakati pa ife, amene ife tinawamva ndi makutu athu; tsopano ife tikumuwona Iye (ndi maso athu) akutanthauzira Mawu Ake Omwe, ife sitikusowa kutanthauzira kulikonse kwa munthu. O mpingo wa Mulungu Wamoyo! pano ndi pa lamya! dzukani mwamsanga, nthawi isanathe!

Tsegulani mitima yanu ndi kumva zimene Mulungu wanena kwa inu, mipingo yake yonse. Tsopano ife tikumuwona IYE, ndi maso athu, AKUTANTHAWUZILA MAWU AKE OMWE. Sitikufuna kutanthauzira kulikonse kwa munthu!! DZUKANI NTHAWI ISANATHE!!

Tamva za zinthu izi moyo wathu wonse zimene zikanati zidzachitike mu nthawi yotsiriza. Tsopano tikuwona ndi maso athu zikuchitika.

Iye anatiuza ife, pali NJIRA IMODZI YOKHA, IYO NDI NJIRA YOPEREKEDWA YA MULUNGU IYE ANAPANGIRA MKWATIBWI WAKE. MUYENERA KUKHALA NDI LIWU LA MULUNGU PA TEPI.

Ndikuitana dziko kuti libwere kudzalumikizana nafe Lamlungu pa 12:00 p.m., nthawi ya ku Jeffersonville, ndi kumva Njira yoperekedwa ndi Mulungu ya lero. Ndiye inunso mukhoza kunena kuti, “Ndamva za Inu, koma tsopano ndikukuonani inu”.

M’bale. Joseph Branham

Uthenga: 65-1127E Ine Ndakhala Ndikumva Koma Tsopano Ine Ndawona

Malemba

Genesis 17
Eksodo 14:13-16
Yobu chaputala 14 ndi 42:1-5
Amosi 3:7
Marko 11:22-26 ndi 14:3-9
Luka 17:28-30