25-0323 Chisindikizo Chachiwiri

Uthenga: 63-0319 Chisindikizo Chachiwiri

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa Omvetsera tepi,

Funso: Kodi tili mu Chifuniro Chake changwiro posewera Matepi?
Yankho: INDE.

Funso: Kodi Mkwatibwi akusowa zambiri kuposa zomwe zanenedwa pa Matepi?
Yankho: AYI.

Funso: Kodi tikuphonya kena kake pomvetsera Matepi OKHA?
Yankho: AYI.

Funso: Kodi tingakhale Mkwatibwi pongomvetsera Matepi OKHA?
Yankho: MOTSINDIKA KWAMBIRI, INDE!

Tsopano kumbukirani, “Palibe choti chiwululidwe; Mulungu sadzachita kanthu, nkonse, mpaka poyamba Iye atawulula icho kwa antchito Ake, aneneri.”

Kotero, ZONSE zomwe Ife tikufuna zinalankhulidwa ndipo ziri pa matepi; kapena, pamene mngelo Wake wachisanu ndi chiwiri adzabwerera kudziko lapansi, IYE adzatiuza ife pamenepo.

O Mkwatibwi, tiyeni tiwone mwamasomphenya zomwe zikuchitika ndi Mkwatibwi wa Khristu padziko lonse lapansi. Atate akusonkhanitsa Mkwatibwi Wake palimodzi ndi Liwu Lake ndipo likubangula, “Pakuti Atero Ambuye.”

Kumbukirani, iye anatiuza chimene Mabingu anali: “Phokoso lowomba lalikulu la Bingu ndi Liwu la Mulungu”. Ndipo kodi Liwu la Mulungu kwa Mkwatibwi ndi chiyani? Mthenga wa mngelo wachisanu ndi chiwiri wa Mulungu, William Marrion Branham.

Iye anati pakubwera Mabingu asanu ndi awiri achinsinsi amene sanalembedwe nkomwe. Ndipo kuti kupyolera mu Mabingu Asanu ndi awiri awo, izo zidzabweretsa Mkwatibwi palimodzi kwa chikhulupiriro chokwatulitsa.

Mawu a Ambuye amadza kwa aneneri Ake. Ngati Iye akanakhala ndi kachitidwe kabwinoko, Iye akadagwiritsa ntchito iko. Iye anasankha dongosolo labwino kwambiri pachiyambi ndipo Iye sangasinthe, ndipo sadzasintha.

Chotero, Liwu la Mulungu, likuyankhula kupyolera mwa mngelo Wake wachisanu ndi chiwiri, likubweretsa Mkwatibwi Wake palimodzi ndi kutipatsa ife Chikhulupiriro Chokwatulitsa.

Mpingo sunadabwepo kuchokera 1933, kumusi ku mtsinje tsiku lija, kuti William Marrion Branham ndi Liwu la Mulungu, Likubangula, “Pakuti Atero Ambuye,” ndipo anatumizidwa kuyitana, kusonkhanitsa, ndi kutsogolera Mkwatibwi.

Ine ndikufuna kuti ndikuyitaneni inu kuti mubwere kudzamvetsera nafe Lamlungu pa 12:00 p.m., nthawi yaku Jeffersonville, pamene Ambuye wathu Yesu akutsegula Bukhu, akumatula Chisindikizo, ndi kuchitumiza Icho ku dziko lapansi, kwa mngelo Wake wachisanu ndi chiwiri, kuti adzawululire Icho kwa Ife!

M’bale. Joseph Branham

Tsiku: Lamlungu, pa 23 Marichi , 2025
Uthenga: Chisindikizo Chachiwiri 63-0319
Nthawi: 12:00 PM, nthawi yaku Jeffersonville

Malemba oti muwerenge musayambe kumvera Uthenga:
Mateyu woyera 4:8 / 11:25-26 / 24:6
Marko woyera 16:16
Yohane woyera 14:12
2 Atesalonika 2:3
Ahebri 4:12
Chibvumbulutso 2:6/6:3-4/17/19:11-16
Yoweli 2:25
Amosi 3:6-7