25-0202 Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele

Uthenga: 61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa Iwo Osankhidwa,

Ndi nthawi ya dzinja yabwino bwanji yomwe takhala tili nayo tikamaphunzira mibadwo isanu ndi iwiri ya mipingo, kenako Mulungu akuululanso zochuluka kwa ife mu Bukhu la Chibvumbulutso cha Yesu Khristu. Momwe machaputala atatu oyamba a Chibvumbulutso anali mibadwo ya mpingo, kenako momwe Yohane adatengedwera kunka ku mwamba mmutu wa 4 ndi 5 ndikutisonyeza zinthu zomwe zinali mkudza.

Mu mutu wa 6., Iye anaulula momwe Yohane adatsikira dziko lapansi kuti aone zinthu zomwe zikuchitika kuchokera ku mutu wa 6. Kuyambira mutu 19 wa buku la Chivumbulutso.

Mkwatibwi adzakhala wodalitsika bwanji Lamlungu pamene tikumva Liwu la Mulungu likulankhula kudzera mwa mngelo wake Wamphamvu wachisanu ndi chiwiri akutiuza ife chomwe chiti chiwululidwe patsogolo.

Ndine wokondwa kwambiri kunena kuti tsopano tiyamba kuphunzira kwakukulu masabata makumi asanu ndi awiri a Daniel. Mneneri ananena kuti icho chimangilira uthenga wonse tisanapite mu Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri; Malipenga 7; Matsoka atatu; mkazi wovala dzuwa; kutulutsa a m’dierekezi wofiira; handiredi ndi forte-foro sauzande atasindikizidwa apo ; Zonse zikuchitika pakati pa nthawi ino.

Buku la Danieli ndi ndendende kalendala ya m’badwo ndi nthawi yomwe tikukhalamo ino, ndipo chingawoneke chovuta bwanji, Mulungu adzachiswa icho ndikuchipanga icho kukhala chophweka kwa ife.

Ndipo Mulungu akudziwa kuti ndizomwe ndikufuna tsopano, kuti nditonthoze anthu ake ndikuwauza chomwe chili pafupi, Onse a iwo m’mawa uno ndipo kudutsa ku mayiko omwe matepi awa adzapita, Pa dziko lonse lapansi, kuti tili kumapeto a nthawi.

Ndife anthu osankhidwa a Mulungu omwe akukhumba ndi kupempherera tsikulo ndi Ola limenelo. Ndipo maso athu akuyang’anila kumwamba, ndipo tikuyembekezera Iye kudza Kwake.

Tiyeni tonse tikhale ngati Danieli ndikuyang’ana nkhope zathu kumwamba, popemphera ndi mapembedzero, monga tikudziwa pa kuwerenga mawu ndi kumva Liwu lake, Kubwera kwa Ambuye kukuyandikira msanga; Tili kumapeto.

Tithandizeni Atate kuika cholemera chilichonse kumbali, tchimo lililonse, kusakhulupirira kwakung’ono kulikonse komwe kungatibwezere ife mmbuyo. Tsopano tiyeni tikambirane za mayitanidwe apamwamba, podziwa kuti nthawi yathu ndi yochepa.

Uthengawu Wapita kulinkonse. Chilichonse chakonzeka tsopano; Tikuyembekezera ndi kupuma. Mpingo wasindikizidwa. Oipa akuchita zoipa kwambiri. Mipingo ikukhala mpingo wokhuthala, koma oyera anu akubwera pafupi ndi inu.

Tili ndi Liwu likufuula m’chipululu, likuitana anthu kubwerera ku uthenga wa pachiyambi; Kubwerera ku zinthu za Mulungu. Timamvetsetsa mwa vumbulutso izi zinthu zomwe zikuchitika.

Bwerani mudzalumikizane nafe Lamlungu lino nthawi ya 12:00PM nthawi ya ku Jeffersonville , pomwe Mulungu akuwululira Mawu Ake kwa ife, pamene tikuyamba kuphunzira kwakukulu za buku la Danieli.

M’bale. Joseph Branham

61-0730M – Malangizo a Gabriel kwa Daniel