Uthenga: 60-1231 Chibvumbulutso, Mutu Foro Gawo I
- 24-1229 Chibvumbulutso, Mutu Foro Gawo I
- 20-1231 Chibvumbulutso, Mutu Foro Gawo I
- 16-0413 Chibvumbulutso, Mutu Foro Gawo I
Wokondedwa Oyera Ovala Mwinjiro Woyera,
Tikamamva Liwu la Mulungu likuyankhula nafe, chinachake chimachitika mkati mwa moyo wathu. Thupi lathu lonse limasinthidwa ndipo dziko lotizungulira likuwoneka kuti likutha.
Kodi munthu angakhoze bwanji kufotokoza zomwe zikuchitika mu mitima yathu, malingaliro athu, ndi moyo wathu, pamene Liwu la Mulungu livundukula Mawu Ake ndi Uthenga uliwonse umene timamva?
Monga mneneri wathu, timamva kuti takwatulidwira kumwamba kwachitatu ndipo mzimu wathu ukuwoneka kuti ukuchoka mu thupi lachivundi ili. Palibe mawu ofotokozera zomwe timamva pamene Mulungu akutiululira Mawu ake kuposa kale.
Yohane anaikidwa pa chisumbu cha Patmo ndipo anapemphedwa kuti alembe zimene anaona ndi kuziika mu bukhu lotchedwa Chivumbulutso, kotero izo zikanadzapita kupyola mu mibadwo. Zinsinsi zimenezo zakhala zobisika mpaka zidaululidwa kwa ife kupyolera mwa mthenga Wake wosankhidwa wa 7.
Ndiye Yohane anamva Liwu lomwelo pamwamba pa iye ndipo anakwatulidwira kumwamba kwachitatu. Liwu lija linamuwonetsa iye mibadwo ya mpingo, kudza kwa Ayuda, kutsanulidwa kwa miliri, Mkwatulo, Kudza kachiwiri, Zakachikwi, ndi Kwawo Kwamuyaya kwa opulumutsidwa Ake. Iye anamutengera iye mmwamba ndipo anabwereza chinthu chonsecho kwa Yohane monga Iye anati Iye akanadzachita.
Koma kodi Yohane anaona ndani pamene anaona kubwerezako? Palibe amene amadziwa mpaka lero.
Chinthu choyamba chimene anaona pakubwera chinali Mose. Iye anaimira oyera mtima akufa amene adzaukitsidwa; mibadwo isanu ndi umodzi yonse yomwe inagona.
Koma si Mose yekha amene anaima pamenepo, komanso Eliya anali pamenepo.
Kodi Eliya amene anali kuyima anali ndani?
Koma Eliya anali kumeneko; m’thenga wa tsiku lotsiriza, ndi gulu lake, la osandulika, okwatulidwa.
ULEMELERO…HALELUYA…Kodi Yohane adamuwona atayimapo ndani?
Osati wina koma mthenga wa mngelo wa 7 wa Mulungu, William Marrion Branham, ndi GULU LAKE LA OSANDULIKA, OKWATULIDWA… ALIYENSE WA IFE!!
Eliya ankayimira oyeramtima akufa…Ine ndikutanthauza Mose, ndi kuwukitsidwa. Eliya ankayimira gulu losandulika. Kumbukirani, Mose anali woyamba, ndipo kenako Eliya. Eliya anali woti adzakhale mthenga wa tsiku lotsiriza, kuti ndi iye ndi gulu lake kukanadzabwera chiwukitsiro…kukanadzabwera…chabwino, ukanadzabwera Mkwatulo, ine ndikutanthauza. Mose anabweretsa chiwukitsiro ndipo Eliya anabweretsa gulu Lokwatulidwa. Ndipo, pamenepo, onse a iwo anayimiriridwa pomwepo.
Lankhulani za kuvundukula, kuwulula, ndi Chivumbulutso.
Apa Iwo uli! Ife tiri nawo Iwo kumene ndi ife tsopano, Mzimu Woyera, Yesu Khristu, yemweyo dzulo, lero, ndi nthawizonse. Ndinu…Iwo ukulalikira kwa inu, Iwo ukukuphunzitsani inu, Iwo ukuyesera kuti ukufikitseni inu kuti muwone chimene chiri cholondola ndi cholakwika. Ndi Mzimu Woyera Mwiniwake ukuyankhula kupyolera mu milomo ya munthu, ukugwira ntchito pakati pa anthu, kuyesa kusonyeza chifundo ndi chisomo.
Ndife Oyera Ovala Mwinjiro Woyera amene mngelo wake anawaona akuchokera ku dziko lonse lapansi kudzadya Mkate wa Moyo. Tili pa kutomeledwa ndipo wokwatitsidwa ndi Iye ndipo tamva kupsompsona kwa Iye kwa chikwati mu mtima mwathu. Ife tinadzilonjeza tokha kwa Iye, ndi ku Liwu Lake lokha. Tilibe, ndipo sitidzadzidetsa ndi mawu ena aliwonse.
Mkwatibwi akukonzekera kukwera mmwamba monga Yohane anachitira; mu Kukhalapo kwa Mulungu. Tidzakwatulidwa pa Mkwatulo wa Mpingo. Momwe izo zimangozungulira moyo wathu!
Kodi Iye atiululira chiyani motsatira?
Ziweruzo; mwala wa sardine, ndi chimene umaimira; idachita gawo lotani. Yaspi, ndi miyala yonse yosiyana. Iye adzazitenga zonse izi mmusi kupyola mu Ezekieli, kubwerera ku Genesis, kubwerera ku Chivumbulutso, kubwera mmusi pakati pa Baibulo, kuzimangiriza izo palimodzi; miyala yonseyi ndi mitundu yosiyanasiyana.
Ndi Mzimu Woyera womwewo, Mulungu yemweyo, kusonyeza zizindikiro zomwezo, zodabwitsa zomwezo, kuchita chinthu chomwecho basi monga Iye analonjezera. Ndi Mkwatibwi wa Yesu Khristu akudzikonzekeretsa Yekha pakumva Liwu Lake.
Ife tikukulandirani inu kuti mulumikizane nafe pamene ife tikulowa mu malo ammwambamwamba pa 12:00 p.M., nthawi ya Jeffersonville, kuti tidzamve Eliya, mthenga wa Mulungu mu m’badwo wotsiriza uno, akuwulula zinsinsi zimene zakhala zobisika mu mibadwo yonse.
M’bale. Joseph Branham
Uthenga: 60-1231 Chivumbulutso,Mutu Foro Gawo I
Chonde kumbukirani Uthenga wathu wa Chaka Chatsopano, Lachiwiri usiku: Mpikisano 62-1231. Palibe njira yabwinoko yoyambira Chaka Chatsopano.