Uthenga: 60-1211M Anamwali Khumi, Ndi Ayuda Handirede Ndi Forte-Foro Sauzande
- 24-1201 Anamwali Khumi, Ndi Ayuda Handirede Ndi Forte-Foro Sauzande
- 23-0611 Anamwali Khumi, Ndi Ayuda Handirede Ndi Forte-Foro Sauzande
- 20-1220 Anamwali Khumi, Ndi Ayuda Handirede Ndi Forte-Foro Sauzande
- 19-0303 Anamwali Khumi, Ndi Ayuda Handirede Ndi Forte-Foro Sauzande
- 16-0403 Anamwali Khumi, Ndi Ayuda Handirede Ndi Forte-Foro Sauzande
M’mawa Wabwino Abwenzi
Sizinayambe zachitikapo mu mbiri yakale ya dziko pamene M’kwatibwi wa Khristu wochokera kuzungulira dziko anakhoza kulumikizidwa palimodzi mu mgwirizano umodzi, pamene mkokomo wochokera Kumwamba, Liwu lomwe la Mulungu, likanakhoza kubwera mothamanga mkati.
Malemba akukwaniritsidwa. Ndi nthawi yachilumikizano chizindikiro cha Mbewu. Chilumikizano chosawoneka cha Mkwatibwi wa Khristu chikuchitika pamene ife tikukhala pamaso pa Mwana wamwamuna, kucha, kudzikonzekeretsa Yekha pakumva Liwu lomwelo la Mulungu.
Ife tikupangidwa angwiro ndi utumiki Wake wofutukuka pasanu.
Ndi angati amakhulupirira kuti mphatso ndi maitanidwe ziri zopanda kulapa? Baibulo linati pali mphatso zisanu mu mpingo. Mulungu anaika mu mpingo Atumwi, kapena amishonare, atumwi, aneneri, aphunzitsi, avangeli, abusa.
- Mlaliki: Ine ndingapite kumusi mumsewu uko. Ndiye winawake akanati, “Kodi ndiwe mlaliki?” Ine ndikanati, “Inde bwana. Inde, ndine mlaliki.”
- Mphunzitsi: Ndipo tsopano chifukwa chimene ine sindinayambe ndalalikira mmawa uno, chinali chifukwa, ine ndinaganiza, pophunzitsa, ife tikanamvetsa izo bwinoko kuposa kungotenga mutu ndi kuwulumpha iwo. Ife tikanangophunzitsa izo.
- Mtumwi: Mawu akuti “mmishonale” amatanthauza “m’modzi wotumizidwa.” “Mtumwi” amatanthauza “mmodzi wotumidwa.” Mmishonale ndi mtumwi. Ine—ine, ndine mmishonare, monga inu mukudziwa, ndimachita uvangeli, ntchito ya umishonare, pafupi kasanu ndi kawiri kutsidya kwa nyanja, kuzungulira dziko.
- Mneneri: Kodi mukundikhulupirira kuti ndine mneneri wa Mulungu? Kenako pita ukachite zimene ndakuuza.
- Abusa: Mukudziwa chimene ndakuchitirani inu? Inu mumanditcha ine m’busa wanu, ndipo inu mukunena bwino, pakuti chotero ine ndiri.
Ndipo ine ndinawawona mamilioni awo atayima pamenepo, ine ndinati, “Kodi onsewo ndi a Branham?” Anati, “Ayi.” Anati, “Iwo ndi otembenuka anu.” Ndipo ine ndinati, ine—ine ndinati, “Ine ndikufuna kumuwona Yesu.” Iye anati, “Ayi. Idzakhala nthawi Iye asanabwerebe. Koma Iye adzabwera kwa inu poyamba ndipo inu mudzaweruzidwa ndi Mawu amene inu munawalalikira,
Ndiye tonse tinakweza manja athu ndi kunenabkuti, “Ife tikupumura pa icho!”
Chinachake chikukonzekera kuti chichitike. Chikuchitika ndi chiyani? Akufa mwa Khristu ayamba kuwuka pozungulira ine. Ndikumva kusintha kwabwera mthupi langa. Tsitsi langa la Imvi, lapita. Yang’anani nkhope yanga … makwinya anga onse atha. Zopsinja zanga ndi zowawa …. ZAPITA. Maganizo anga ankhawa atha nthawi yomweyo. Ndasinthidwa mu m’kamphindi, mu m’kuphethira kwa diso.
Kenako tidzayamba kuyang’ana pozungulira ife ndikuwona okondedwa athu. O mai, pali Amayi ndi Abambo…Ulemelero, mwana wanga wamamuna…mwana wanga wamkazi. Agogo amuna, Agogo akazi, oh ndinakusowani nonse. Hei … pali mzanga wakale. O TAWONANI, ndi M’bale Branham, mneneri wathu, Aleluya!! Ndi pano. Zikuchitika!
Ndiye palimodzi, zonse mwakamodzi, ife tidzakwatudwira kutali kwinakwake mu mlengalenga kuseri kwa dziko lapansi. Tidzakomana ndi Ambuye panjira Yake yotsika. Ife tidzayima pamenepo ndi Iye pa mphete za dziko lapansi ndi kuyimba nyimbo za chiwombolo. Tidzayimba ndi kumuyamika Iye chifukwa cha chisomo Chake chachiwombolo chimene Iye watipatsa ife.
Zonse zomwe zili munkhokwe ndiza Mkwatibwi Wake. Ndi nthawi yanji yomwe ife titi tidzakhale nayo kunthawi zamuyaya wina ndi mzake, ndi Ambuye wathu Yesu. Mawu achivundi sangakhoze kufotokoza, Ambuye, momwe ife tikumvera mu mitima yathu.
Ngati inu mukufuna kuti mumumve Iye akukuitanani inu Mkwatibwi Wake, ndi kukuuzani inu momwe izo ziti zidzakhalire ndi Iye, bwerani muzajoinane nafe Lamulungu lino pa 12:00 P.M., nthawi yaku Jeffersonville, ndipo inu mudzadalitsidwa mopitirira muyeso.
M’bale. Joseph Branham
60-1211M – Anamwali Khumi, Ndi Ayuda Handirede Ndi Forte-Foro Sauzande