CILAMULO CA NCHITO YAKUMASULIRA PA BRANHAM TABERNACLE

Kumasulila kwa mapemphero kumacitidwa mkati mwamapemphero ndi sagwirisidwa kuti akhale cimasuliro co wonjezedwa, mkamasulidwe,kapena kupangidwanso munjira ina iriyonse. Omasulira ali ndi cholinga cabwino kungo tsatila mwaceru comwe cikunenedwa panthawi iriyonse yamapemphero , koma kudzakhala kuphonya mau ndi zophonyeka munthu zomwe sangathe kupewa mkati mwakasulira. Mauthenga omasulidwa ALIBE cholinga kuti akhale cimasuliro Colima paokha , ndipo SIALI ofikapo pamulingo wakujambula Kwa Voice of God.

Colinga cathu comasulila mau ndi kupeleka mpata kwa iwo omwe salankhula Cingelezi kuti tizimphera limodzi nthawi ya mapemphero. Mpingo wa Branham Tabernacle ndi wa nzeru zanchito ya cimishonali yomwe ibvutikira mkwatibwi wa Khristu m’minda ya cimishoni mozungulira dziko lonse la pansi. Ife ndife othokoza pampata omwe ambuye atipasa kuti tiwafike iwo kupyolera m’mapemphero athu ,cikondi cozipeleka ,ndi tsopano ciyanjano pa mau kupyolera njira yo lumikizana. Tikukhulupila kuti mapemphero awa adzakhala daliso Kwa inu ndi banja lanu. Chidziwitso ici cinapangidwa mogwirizana ndi Branham Tabernacle

An Independent Church of the WORD